2018 Dapp Chichewa Mock

Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 6

EXAMINATION NUMBER: _________________________

DAPP 400 PRIMARY SCHOOL MOCK EXAMINATIONS


2018 PRIMARY SCHOOL LEAVING CERTIFICATE EXAMINATION

CHICHEWA
(100 MALIKISI)

SUBJECT NUMBER: P032

TIME ALLOWED: 2hr 15 min.

DZINA: ……………………………………………………………………………………………..…
DZINA LA SUKULU: ………………………………………………………………………………..
MALANGIZO:
1. Pepala ili lili ndi magawo anayi: A, B, C ndi D.
2. Lembani dzina lanu ndi dzina la sukulu yanu pamwamba pa tsamba lino.
3. Lembani chimangirizo kapena kalata mu Gawo A ndipo muyankhe mafunso onse mu Gawo B, C ndi D.
4. Yankhani mafunso a mu Gawo B ndi C m’mipata yomwe yaperekedwa pansi pa funso lililonse.
5. Yankhani mafunso a mu Gawo D pozunguliza lemba lokhonza pafunso lililonse.

GAWO A (MALIKSI 30)


Langizo:
 Yankhani funso limodzi mwa mafunso awiri alim’musiwa
 Sankhani mutu wa chimangirizo kapena kalata
 Mawu a chimangirizo chanu kapena kalata yanu asachepere 100 asaposere150

1. Lembani chimangirizo pa mutu woti “KUSAMALIRA NTHAKA”. Mwa zina tsatani izi polemba
chimangirizo chanu:
Ndime yoyamba:
 Kufunika kwa nthaka.
 M’mene anthu amaonongera nthaka.
Ndime yachiwiri:
 Mavuto omwe akudza chifukwa choononga nthaka
 Mmene tingasamalire nthaka
Ndime yachitatu:
 Ubwino osamala nthaka.
 Magulu ndi mabungwe omwe akuthandizirapo kusamalira nthaka
Kapena
2. Lembani kalata kwa amalume anu omwe amakhala kutawuni yowafotokozera kuti akuchotsani sukulu
kaamba kophwanya malamulo.
Mwa zina tsatani izi polemba kalata yanu:
Ndime yoyamba:
 Tsiku Lomwe anakuchotsani sukulu.
 Chifukwa chomwe anakuchotserani sukulu.
Ndime yachiwiri:
 Fotokozani zomwe zinachitika kuti akuchotseni sukulu
 Ndani anakupeza kuti aphunzitsi aziwe za nkhaniyi?
 Udamva bwanji mu mtima mwako panthawi imeneyi?
Ndimeyachitatu
 Kuchotsedwa kwanu pa sukulu kwakhuza motani maphunziro anu?
GAWO B (MALIKSI 20)

3.Werengani nkhani yotsatilayi mosamala kenaka yankhani mafunso otsatilawo.

Anyamata ndi atsikana amapita sukulu kukaphunzira zinthu zambiri monga; ukhondo, khalidwe labwino ndi
kutsatira malamulo.

Ukhondo amaphunzira kuti azipewa matenda ndi kukhala ndi moyo wa nthanzi. Umve umazetsa tizilombo
tomwe timayambitsa matenda omwe munthu ukhonza kufa nawo

Ana amaphunziranso za makhalidwe abwino. Izi zimawathandiza kulemekeza makolo awo ndi anthu ena.
Kusukulu ana amaphunzira mosiyanasiyana.Ana ena amalimbikira sukulu ena amachita ulesi. Ana aulesi
kawirikawiri amalephera mayeso pomwe olimbikira komanso achangu amakhonza mayeso

Chinthu chomwe mwana wasukulu aliyense ayenera kuziwa ndi chakuti kusukulu kulibe kapolo kapena
mfulu. Kawirikawiri kusukulu kumapezeka anyamata ena kapena atsikana omwe amavutitsa amzawo
achilendo. Kusukulu kumene kuli aphunzitsi oziwa udindo wawo, ana ozunza anzawowa amalangidwa.
Kuzunza munthu opanda chifukwa ndi khalidwe la upandu. Koma kukoma mtima ndi chinthu chofunika
kwambiri popeza kumaonetsa kusiyana pakati pa anthu ndi nyama.

Mwana wa sukulu sayenera kukwatira kapena kukwatiwa. Ili ndi limodzi mwa malamulo
apasukulu.Malamulo amatchinjiriza ophunzira ngakhale ophunzirawo amaganiza kuti malamulo
amachepetsa ufulu wawo. Aphunzitsi ayenera kufotokozera ophunzirawo ubwino wotsatira malamulo
popewa kuti patsogolo angazanong’oneze bondo.

MAFUNSO
Tsopano yankhani mafunso otsatilawa pa mizere ili pansi pa funso lililonse.
a. Perekani zinthu ziwiri zomwe anyamata ndi atsikana amaphunzira kusukulu.
_____________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________________
(2malikisi)
b. Kodi ukhondo ndi ofunika bwanji?
______________________________________________________________________ (1 malikisi)
c. Tizilombo toyambitsa matenda timabwera bwanji?
_____________________________________________________________________________
(1malikisi)
d. Nchifukwa chayani ophunzira ena amalephera mayeso?
______________________________________________________________________ (1 malikisi)
e. Lembani khalidwe loipa lomwe ophunzira ena amakhala nalo kusukulu.
_____________________________________________________________________ _ (2 malikisi)
f. Perekani matanthauzo amawu awa:
i. Uve:
_____________________________________________________________________
(1malikisi)
ii. Achilendo:
_____________________________________________________________________
(1malikisi)
iii. Kutchinjiriza:
_____________________________________________________________________
(1malikisi)
g. Ndi aphunzitsi otani omwe amapereka chilango kwa ana akhalidwe loyipa?
______________________________________________________________________ (2 malikisi)
h. Kodi kukoma mtima ndi kofunika bwanji?
______________________________________________________________________ (2 malikisi)
i. Perekani tanthauzo la chining’a ichi; “angazanong’oneze bondo”
______________________________________________________________________ (2 malikisi)
j. Nchifukwa chiyani ophunzira amadana ndi malamulo pa sukulu?
_____________________________________________________________________ (2 malikisi)
k. Perekani mutu wa nkhaniyi:
______________________________________________________________________ (2 malikisi)

GAWO C (MALIKISI 10)


4. Yankhani mafunso onse awiri am’gawo lino.

A. Werengeni kankhanika ndipo muyankhe mafunso otsatirawo

“Pepani anamalira nonse!


Pepani Gogo Chalo!
Pepaninso amfumu Zaonaife ndi mafumu anzanu onse!
Pepani amayi ndi abambo , anyamata ndi asungwana nonse!
Tsopano tifuna tiyambepo mwambo wa zovutazi. Choncho, tiyeni tikhale chete tonse kuti tipereke ulemu
woyenera komanso timvane. Tidziwa zovuta zilibe chizolowezi. Nanga tingatani poti ndi mmene
kudalengedwera. Motero, pepani,pepani, anamalira nonse tiugwire mtima wathu”.

Mafunso
i. Kodi mawu amenewa angayankhule ndi ndani?
_______________________________________________________________________________
(Malikisi 1)

ii. Kodi malonjewa amaperekedwa pa mwambo wanji?


_______________________________________________________________________________
(Malikisi 1)

iii. Kodi zimatanthauza chiyani anthu akaika Masamba pamsewu kumudzi?


_______________________________________________________________________________
(Malikisi 1)
iv. Perekani matanthauzo a mawu awa
(i) Gogo Chalo_________________________________________________________ (Malikisi 1)
(ii) Zovuta ______________________________________________________________ (Malikisi 1)

B. Kupanga ziganizo
Pangani ziganizo zomveka bwino ndi mawu awa:

i. Bwenzi la mphasa:
_______________________________________________________________________ (Malikisi 1)

ii.Tsoka
_______________________________________________________________________ (Malikisi 1)

iii.Waulesi
_______________________________________________________________________ (Malikisi 1)

iv.Buu!!
_______________________________________________________________________ (Malikisi 1)
v.Kalilore
_______________________________________________________________________ (Malikisi 1)

GAWO D (MALIKISI 40) Mafunso 16 mpaka 18 sankhani mitundu


Zungulizani yankho lolondola (A, B, C ndi D) yanthambi yachiganizo yomwe ili ndi mzere kunsi
m’mafunso otsatilawa: kwake:

Mafunso 6 mpaka 10 sankhani mitundu ya mawu 16. Iye walandira kalata yoti akavotere.
amene atsekedwa mzere kunsi kwawo mziganizo a. yadzina c. yamuonjezi
zotsatirazi: b. yamfotokozi d. yoima payokha.

6. Zanga zidatha zulo. 17. Mfumu idawadzudzula chifukwa amasakaza


a. mneni c. mlowam’malo nkhalango.
b. mlumikizi d. mfotokozi a. yamfotokozi c. yadzina
b. yoima payokha d. yamuonjezi
7. M’nyamata akufuna ntchitoyo ngotani?
a. mfotokozi c. muonjezi 18. Iyi ndi sukulu imene ndidaphunzirapo.
b. dzina d. mvekera a. nthambi yoima payokha c. yadzina
b. yamuonjezi d. yamfotokozi
8. Choka! Sindifuna kukuona.
a. mvekero c. mlowam’malo Mafunso 19 mpaka 23: Sakhani mawu ofanana
b. mfuu d. muonjezi m’matanthauzo ndi omwe ali ndi mzere kunsi
kwawo:
9. Maliya walandira uphungu woyenera.
a. mfotokozi c. mvekero 19. Iye ndi njinga.
b. mlowam’malo d. dzina a. chimasomaso c. waulemu
b. wofatsa d. wachinsisi
10. Iye ndi mbava.
a. mneni c. muonjezi 20. Adatha zilumika ziwiri alibe mwana.
b. mperekezi d. mlumikizi a. masiku c. zipika
b. miyezi d. zaka
Mafunso 11 mpaka 15 sankhani mitundu ya
afotokozi yomwe ili ndi mzere kunsi kwake 21. Maliya adali mzime m’banja lathu.
m’ziganizo zotsatirazi: a.wachiwiri c. chisamba
11. Kaziputa adakwatira mkazi wokongola. b. chitsitsa msepe d. wamkulu
a. wakuchuluka c. wamaonekedwe
b. waumwini d. wamgwirizano 22. Anamulangeni adakatola nkhuni ku dondo
a. phiri c. chipululu
12. Awa ndi aphunzitsi amene tili nawo pano. b. dambo d. nkhalango
a. woloza c. wakuchuluka
b. wamgwirizano d. waumwini 23. Atate adakhala pa chikumba.
a. mphasa c. mkeka
13. Ali ndi khutu limodzi mzangayi. b. chikopa d. pansi
a. wamgwirizano c. wamaonekedwe
b. wachimzake d. wakuchuluka Mafunso 24 mpaka 28: Sankhani magulu a
maina m’mawu otsatirawa:
14. Bambo aja akudwala edzi.
a. woloza c. wofunsira 24. Nkhwangwa
b. waumwini d. wowerenga a. I-, Zi- c. U-, Ma-
b. Li-, Ma- d. Mu_,A
15. Tikatere tithe kuunikira zasukulu yathu ino.
a. wadzina c. waumwini
b. woloza d. wofunsira. 25. Thabwa.
a. Chi-, Zi- c. U-, Ma- d. papsa tonola suziwa mtima wamoto
b. I-, Zi- d. Li, Ma-
36. Pawiripawiri sipauzirika
26. Ufulu A. ovala nyanda salumpha moto
a. Li-, Ma- c. Mu-, A- B. mapanga awiriavumbwitsa
b. Mu-, Mi- d. U-, Ma- C. chisoni chidaphetsa nkhwali
D. fumbi ndiwe mwini
27. Chimanga
a. I-, Zi- c. Mu-, A- 37. Wakwata kwamphezi saopa kung’anima
b. Chi-, Zi- d. Ka-, Ti- a. chala chimodzi sichiswa nsabwe
b. khoswe wapadzala adaulura wapatsindwi
28. Waya c. walira mvula walira matope
a. Mu-, Mi- c. Chi-, Zi- d. ichi chakoma ichi chakoma pusi adagwa
b. Mu-, A- d. Li-, Ma- chagada

Mafunso 29 mpaka 31: Sakhani maina a Mafunso 38 mpaka 40: Sankhani msintho wa
zazimuna za maina otsatirawa: aneni omwe ali ndi mzere kunsi kwawo:
29. Nkhunda
a. tambala c. mkota 38. Nyimbo idaimbidwa bwino
b. chipsolopsolo d. mzambwe a. ochitidwa c. ochititsitsa
b. ochititsa. d. obwerezabwereza
30. Nkhosa
a. mphulu c. chiunda 39. Nsabwe yoyendayenda idakumana ndi chala
b. thadzi d. tonde a. ochitidwa c. obwerezabwere
b. ochititsitsa d. ochititsa
31. Thadzi
a. tatavyala c. mkota 40. Anyani akumenyana
b . tambala d. mkwati a. ochitira c. otsutsana
b. ochitirana d. ochititsa
Mafunso 32 mpaka 34: Sankhani mayankho a
zilapi zotsatirazi: Mafunso 41 mpaka 45: Sankhani ntchito za
mayina omwe ali ndi mzere kunsi kwawo:
32. Chivunda kunja nyama mkati……………..
a. malambe c. nthutumba 41. Ona mvuu, Basowelo.
b. maso d. lilime a. mwininkhani c. loitanira
b. pamtherankhani d. mtsirizo wa mneni
33. Udzu wamera pa thanthwe…………………
a. mwala c. kapinga 42. Njoka yaluma ng’ombe
b. ndevu d. minga a. loitanira c. lapadera
b. mwininkhani d. panthera nkhani
34. Kamwana kakang’ono ufiti thoo!!…………...
a. mfiti yayikazi c. tsabola 43. Yohane akusewera mpira.
b. moto d. tameki a. pantherankhani c. mtsiriza mawu
b. mwininkhani d. lapadera
Mafunso 35 mpaka 37: Sankhani mikuluwiko
yofananirako m’matanthauzo ndi mikuluwiko 44. Nansani, kathyali ali m’mudzimuno lero.
yotsatirayi: a. lapadera c. pantherankhani wa mperekezi
b. loitanira d. pantherankhani
35. Likaomba otheratu.
a. mvula ikagwakuchuluka zoliralira 45. Dalo adabadwira m’banja losauka.
b. chala chimodzi sichiswa nsabwe a. loitanira c. mwininkhani
c. mapanga awiri avumbwitsa b. lapadera d. patherankani

MAFUNSO ATHERA PAMENEPA!!!!

You might also like