September 9-October 6, 2024: Nkhani Zophunzira Kuyambira

Download as pdf or txt
Download as pdf or txt
You are on page 1of 32

JULY 2 0 24

34567

NKHANI ZOPHUNZIRA KUYAMBIRA:


SEPTEMBER 9–OCTOBER 6, 2024
NKHANI
YOPHUNZIRA 27

Muzikhala Olimba
Mtima Ngati Zadoki
NYIMBO NA. 73
Tithandizeni Kukhala “Zadoki [anali] mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima.”
Olimba Mtima —1 MBIRI 12:28.

ZIMENE TIPHUNZIRE YEREKEZERANI kuti mukuona gulu la anthu oposa 340,000


Tiona mmene chitsanzo omwe asonkhana kuti amuike Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.
cha Zadoki chingatithandi- Kwa masiku atatu, m’dera la mapiri pafupi ndi ku Heburoni kuku-
zire kuti tikhale olimba mveka phokoso la kulankhulana kwa anthu, kuseka komanso
mtima. nyimbo zotamanda. (1 Mbiri 12:39) Pagulu la anthulo pali wachi-
nyamata wina dzina lake Zadoki yemwe sanali wodziwika kwa
anthu ambiri. Koma Yehova anafuna kuti tidziwe zoti iye anali pa-
gululi. (Werengani 1 Mbiri 12:22, 26-28.) Kodi Zadoki anali
ndani?
2 Zadoki anali wansembe amene ankagwira ntchito ndi Abiyata-

ra yemwe anali mkulu wa ansembe. Zadoki anali wamasomphenya


yemwe ankatha kuzindikira zimene Mulungu akufuna ndipo ana-
patsidwa nzeru zapadera. (2 Sam. 15:27) Anthu akafuna malangi-
zo anzeru ankapita kwa Zadoki. Iye analinso munthu wolimba
mtima. Munkhaniyi, tikambirana kwambiri za khalidwe lake lime-
neli.
3 M’masiku otsiriza ano, Satana akuukira kwambiri anthu a Mu-

lungu. (1 Pet. 5:8) Tiyenera kukhala olimba mtima pamene tiku-


yembekezera kuti Yehova awononge Satana ndi dziko loipali.
(Sal. 31:24) Tiyeni tikambirane njira zitatu zomwe tingatsanziri-
re kulimba mtima kwa Zadoki.
1-2. Kodi Zadoki anali ndani? (1 Mbiri 12:22, 26-28)
3. (a) N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova ayenera kukhala olimba mtima?
(b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2
Kodi inuyo mudzatani anthu ena akamakambirana nkhani zandale?
(Onani ndime 4)

MUZIKHALA KUMBALI YA lala kuti Davide waikidwa kukhala mfumu. Ana-


UFUMU WA MULUNGU pita kumeneko atanyamula zida zake koma-
4 Anthu a Yehovafe timayesetsa kukhala ku- nso ali wokonzeka kumenya nkhondo. (1 Mbiri
mbali ya Ufumu wa Mulungu. Koma kuchita zi- 12:38) Iye anali wofunitsitsa kuthandiza Davide
menezi kumafuna kuti tikhale olimba mtima. pa nkhondo yolimbana ndi adani a Isiraeli. Nga-
(Mat. 6:33) Mwachitsanzo, m’dziko loipali ti- khale kuti mwina Zadoki analibe luso lomenyera
mafunika kukhala olimba mtima kuti tizitsatira nkhondo, koma anali wolimba mtima.
6 Kodi Zadoki, yemwe anali wansembe, ana-
mfundo za makhalidwe abwino za Yehova ko-
manso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. phunzira kuti kukhala wolimba mtima? Iye
(1 Ates. 2:2) Timafunikanso kulimba mtima kuti ankakhala ndi anthu omwe anali amphamvu ko-
tisalowerere ndale m’dzikoli, limene anthu ake manso olimba mtima. Ndipo zitsanzo zawo zina-
ndi osagwirizana. (Yoh. 18:36) Atumiki ambiri a muthandiza kwambiri. Mwachitsanzo, kulimba
Yehova akukumana ndi mavuto azachuma, ama- mtima kwa Davide pamene ‘ankatsogolera Aisi-
zunzidwa ndipo ena amaikidwa m’ndende chifu- raeli kunkhondo,’ kunalimbikitsa Aisiraeli onse
kwa chokana kulowerera ndale kapena kulowa kuti akhale kumbali yake. (1 Mbiri 11:1, 2) Ntha-
usilikali. wi zonse Davide ankadalira Yehova kuti amu-
5 Zadoki sanapite ku Heburoni kukangosanga- thandize polimbana ndi adani ake. (Sal. 28:7;
Werengani Salimo 138:3.) Panali amuna ena-
4. N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amafunika kuli- nso amene anathandiza Zadoki kukhala woli-
mba mtima kuti akhale kumbali ya Ufumu wa Mulungu? mba mtima. Mwachitsanzo, panali Yehoyada ndi
(Onaninso chithunzi.)
5. N’chifukwa chiyani Zadoki ankafunika kukhala woli- 6. Kodi chitsanzo chabwino cha Davide chinathandiza
mba mtima kuti athandize Davide? bwanji Zadoki? (Salimo 138:3)

JULY 2024 3
Davide anatuma Zadoki kuti agwire ntchito yomwe ikanaika moyo wake pangozi
(Onani ndime 9)

mwana wake Benaya yemwe anali msilikali wa- MUZITHANDIZA ABALE ANU
mphamvu, ndiponso atsogoleri 22 omwe anali 8 Nthawi zonse anthu a Yehova amathandi-
kumbali ya Davide. (1 Mbiri 11:22-25; 12:26-28) zana. (2 Akor. 8:4) Komabe iwo nthawi zina
Anthu onsewa anasankha kukhala kumbali ya amafunika kulimba mtima kuti achite zimene-
Davide ndi ufumu wake. zi. Mwachitsanzo kukakhala nkhondo, akulu
7 Timalimbikitsidwa komanso kupeza mpha-
amazindikira kuti abale ndi alongo awo ama-
mvu tikamaganizira zitsanzo za anthu omwe funika kulimbikitsidwa, kupatsidwa zinthu zo-
molimba mtima anatsimikiza kukhala kumbali funika pa moyo komanso chakudya chauzimu.
ya ulamuliro wa Yehova. Mwachitsanzo, Mfu- Chifukwa chokonda nkhosa, iwo amalolera kui-
mu yathu Khristu Yesu anakanitsitsa kulowerera ka moyo wawo pangozi kuti apereke thandizo
ndale m’dziko la Satanali. (Mat. 4:8-11; Yoh. lofunika kwa abale awo. (Yoh. 15:12, 13) Akama-
6:14, 15) Nthawi zonse ankadalira Yehova kuti chita zimenezi amakhala akutsanzira Zadoki pa
amupatse mphamvu. Palinso zitsanzo za masi- nkhani ya kulimba mtima.
ku ano za achinyamata ambiri omwe anaikidwa 9 Moyo wa Davide unali pangozi. Mwana wake
m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupirira Abisalomu anali atatsimikiza kuti alande ufumu.
komanso kukana kulowerera ndale. Mungachite (2 Sam. 15:12, 13) Apa Davide ankafunika ku-
bwino kuwerenga nkhani zawo pa jw.org.1 choka ku Yerusalemu mwamsanga. Iye anauza
1 Onerani pa jw.org vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Akhristu
atumiki ake kuti: “Konzekani msangamsanga!
Oona Amafunika Kulimba Mtima—Kuti Asamalowerere Ndale?
8. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe akulu angafunike kuli-
7. (a) Kodi ndi zitsanzo zamasiku ano ziti zomwe zinga- mba mtima kuti athandize abale awo?
tithandize kukhala olimba mtima? (b) Mogwirizana ndi vi- 9. Mogwirizana ndi 2 Samueli 15:27-29, kodi Davide ana-
diyo, kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha M’bale pempha Zadoki kuti achite chiyani? (Onaninso chithu-
Nsilu? nzi.)

4 NSANJA YA OLONDA
Tiyeni tithawe, chifukwa palibe amene anga- reka malangizo omenyera nkhondo omwe aka-
pulumuke m’manja mwa Abisalomu.” (2 Sam. napereka mpata kwa Davide kuti akonzeke. Ke-
15:14) Pamene atumiki akewo ankachoka, Da- nako Husai anauza Zadoki ndi Abiyatara zimene
vide anazindikira kuti pankafunika kuti mu- anakonzazo. (2 Sam. 17:8-16) Choncho amuna
nthu wina atsale kuti azimuuza zimene Abisa- awiriwa anatumiza uthenga kwa Davide. (2 Sam.
lomu angakonze. Choncho anatumiza Zadoki 17:17) Yehova anathandiza Zadoki ndi ansembe
ndi ansembe ena mumzindawo kuti akagwire enawo kuti ateteze Davide.—2 Sam. 17:21, 22.
ntchito imeneyi. (Werengani 2 Samueli 15:27- 11 Ngati mutapemphedwa kuti muthandize
29.) Iwo ankafunika kuchita zinthu mosamala
abale anu pa nthawi yovuta, kodi mungasonyeze
kwambiri chifukwa zimene Davide anawauza ku-
kachitazi, zinali zoopsa komanso zoika moyo bwanji kulimba mtima ngati Zadoki? (1) Mu-
wawo pangozi. Abisalomu anali wankhanza, wo- zitsatira malangizo. Pa nthawi ngati imeneyi,
dzikonda komanso anachitira chinyengo bambo mumafunika kuchita zinthu mogwirizana. Mu-
ake enieni. Ndiye tangoganizani zimene akana- yenera kutsatira malangizo ochokera ku ofesi
chita akanadziwa kuti Zadoki ndi ansembe ena- ya nthambi. (Aheb. 13:17) Nthawi ndi nthawi,
wo anatsala n’cholinga choti akhale akazitape a akulu ayenera kumaonanso zimene anakonza
Davide. pa nkhani yokonzekera ngozi komanso ku-
10 Davide anapempha Zadoki komanso mnza- tsatira malangizo a gulu pa nthawi ya ngozi-
ke wina wokhulupirika dzina lake Husai kuti yo. (1 Akor. 14:33, 40) (2) Muzikhala olimba
amuthandize pa nkhaniyi. (2 Sam. 15:32-37) mtima koma muzichita zinthu mosamala. (Miy.
Potsatira malangizowo, Husai anachititsa kuti 22:3) Muziganiza kaye musanachite zinazake.
Abisalomu ayambe kumukhulupirira. Iye anape-
11. Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Zadoki
10. Kodi Zadoki ndi anzake anateteza bwanji Davide? tikamathandiza abale athu?

Pa nthawi yovuta, muzithandiza abale anu molimba mtima


koma muzichita zinthu mosamala
(Onani ndime 12-13)
Muziyesetsa kuti mukhale otetezeka. (3) Muzi- kutifooketsa ndi pamene wachibale kapena
dalira Yehova. Muzikumbukira kuti Yehova ama- mnzathu wasiya kutumikira Yehova. (Sal. 78:40;
kukondani inuyo komanso abale anuwo. Cho- Miy. 24:10) Ngati timamukonda kwambiri mu-
ncho angakuthandizeni kuti mupereke thandizo nthuyo, zimakhalanso zovuta kwambiri kuti ti-
kwa abale anuwo muli otetezeka. vomereze zimene zachitikazo. Ngati inunso zi-
12 Taganizirani chitsanzo cha Viktor ndi Vita-
menezi zinakuchitikirani, kukhulupirika kwa
lii, abale awiri amene ankagwira ntchito yope- Zadoki kungakulimbikitseni.
reka chakudya ndi madzi kwa Akhristu anza- 15 Zadoki anasankha kukhalabe wokhulupiri-
wo ku Ukraine. Viktor anati: “Tinkasakasaka ka kwa Yehova pamene mnzake Abiyatara ana-
chakudya kwina kulikonse. Nthawi zambiri ti-
sankha kuchita zinthu mosakhulupirika. Izi zi-
nkamva anthu akuomberana chapafupi. M’bale
nachitika kumapeto kwa ulamuliro wa Davide.
wina ananena kuti tikatenge chakudya ku shopu
Davide atatsala pang’ono kufa, mwana wake
yake. Chakudya chimenechi chinathandiza ofali-
Adoniya ankafuna kulanda ufumu wake nga-
tsa ambiri kwa kanthawi. Tikulongedza chaku-
dyacho m’galimoto, bomba linagwera pamtunda khale kuti Yehova anali atalonjeza kuti Solomo
wamamita pafupifupi 20 kuchokera pomwe ti- ndi amene adzakhale mfumu. (1 Mbiri 22:9, 10)
nali. Kwa tsiku lonse ndinkapemphera kwa Ye- Abiyatara anasankha kukhala kumbali ya Ado-
hova kuti andithandize kukhala wolimba mtima niya. (Werengani 1 Mafumu 1:5-8.) Pochita
kuti ndipitirize kuthandiza abale anga.” zimenezi, Abiyatara anakhala wosakhulupirika
13 Vitalii anati: “Tinkafunika kulimba mtima kwa Davide komanso Yehova. Kodi mukugani-
kwambiri. Ulendo wanga woyamba tinayenda za kuti Zadoki anamva bwanji ndi zimenezi?
kwa maola 12. Ndinakhala ndikupemphera kwa Kwa zaka zoposa 40, iye ndi Abiyatara anali ata-
Yehova pa ulendo wonsewu.” Vitalii anali woli- gwira ntchito limodzi monga ansembe. (2 Sam.
mba mtima komanso ankachita zinthu mosama- 8:17) Pa nthawi ina iwo anathandizana kusama-
la. Iye ananenanso kuti: “Ndinkapempha Yeho- lira “likasa la Mulungu woona.” (2 Sam. 15:29)
va kuti andipatse nzeru komanso andithandize Poyamba onsewa anali kumbali ya Davide ndi
kukhala wodzichepetsa. Ndinkadutsa misewu ufumu wake ndipo anachita zambiri potumikira
yokhayo yomwe inali yovomerezedwa ndi boma. Yehova.—2 Sam. 19:11-14.
Chikhulupiriro changa chalimba kwambiri poo- 16 Zadoki anakhalabe wokhulupirika kwa Ye-
na mmene abale ndi alongo amachitira zinthu hova ngakhale kuti Abiyatara anachita zosa-
mogwirizana. Iwo ankachotsa zinthu zimene za- khulupirika. Davide sanasiye kumukhulupirira
tchinga mumsewu, kuchotsa ndi kulongedza za- Zadoki. Chiwembu cha Adoniya chitadziwika,
kudya ndi zinthu m’galimoto komanso kutiko-
Davide anasankha Zadoki, Natani ndi Benaya
nzera chakudya ndi malo ogona.”
kuti akadzoze Solomo kukhala mfumu. (1 Maf.
PITIRIZANI KUKHALA 1:32-34) Kukhala pakati pa atumiki a Yeho-
OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA va okhulupirika monga Natani ndi ena omwe
Chimodzi mwa zinthu zimene zimayesa
14 anali kumbali ya Mfumu Davide, kuyenera kuti
kwambiri chikhulupiriro chathu komanso
15. N’chifukwa chiyani Zadoki ankafunika kukhala oli-
12-13. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Viktor ndi Vitalii? mba mtima kuti apitirize kukhala wokhulupirika kwa Ye-
(Onaninso chithunzi.) hova? (1 Mafumu 1:5-8)
14. Kodi zimatikhudza bwanji munthu amene timamuko- 16. Kodi n’chiyani chinathandiza Zadoki kuti akhalebe
nda akasiya kutumikira Yehova? wokhulupirika?

6 NSANJA YA OLONDA
ndi kumene kunamulimbikitsa Zadoki. (1 Maf. akuonetsetsa kuti pamene ine ndafooka, mka-
1:38, 39) Solomo atakhala mfumu, anasankha zi wanga akhale ndi mphamvu, ndipo pamene
“wansembe Zadoki kuti alowe m’malo mwa Abi- iye wafooka, ine ndikhale ndi mphamvu.” Sidse
yatara.”—1 Maf. 2:35. anawonjezera kuti: “Sitikanakwanitsa kupirira
17 Kodi tingamutsanzire bwanji Zadoki? Ngati zikanakhala kuti Yehova sanatipatse mphamvu
munthu amene mumamukonda wasiya kutumi- zomwe tinkafunikira. Ndinkavutika ndi maga-
kira Yehova, inuyo muzisonyeza kuti mukufuna nizo oona kuti ineyo ndi amene ndinachititsa
kukhalabe wokhulupirika. (Yos. 24:15) Yehova zonsezo, choncho ndinkamuuza Yehova mme-
adzakupatsani mphamvu komanso kukulimbiki- ne ndinkamvera. Pasanapite nthawi yaitali, ku-
tsani. Muzimudalira popemphera kwa iye koma- nabwera mlongo wina yemwe panali patatenga
nso kupitiriza kukhala pa ubwenzi ndi Akhristu zaka zambiri tisanaonane. Anandigwira m’ma-
anzanu okhulupirika. Yehova amaona kukhu- pewa n’kundiyang’ana ndipo anandiuza kuti,
lupirika kwanu ndipo adzakupatsani mphoto. ‘Sidse kumbukira kuti vuto si iweyo.’ Mothandi-
—2 Sam. 22:26. zidwa ndi Yehova, ndakwanitsa kupitiriza ku-
18 Taganizirani zomwe zinachitikira Marco ndi
mutumikira mosangalala.”
mkazi wake Sidse, omwe ana awo awiri aa- 19 Yehova amafuna kuti atumiki ake onse
kazi anasiya choonadi. Marco anati: “Makolo azikhala olimba mtima ngati Zadoki. (2 Tim.
amakonda ana awo kungochokera pamene aba- 1:7) Komabe amafuna kuti tisamangodalira
dwa. Iwo amachita chilichonse chomwe anga- mphamvu zathu. Iye amafuna kuti tizimuda-
the kuti awateteze. Choncho akasankha kusi- lira. Choncho mukakumana ndi zinthu zina
ya kutumikira Yehova zimakhala zopweteka
zofuna kuti musonyeze kulimba mtima,
kwambiri.” Iye ananenanso kuti: “Koma Yehova
muzimupempha kuti akuthandizeni. Musama-
wakhala akutithandiza kuti tipirire. Iye wakhala
kayikire kuti iye adzakuthandizani kuti mukhale
17. Kodi mungatsanzire bwanji Zadoki ngati munthu ye- olimba mtima kwambiri ngati Zadoki.—1 Pet.
mwe mumamukonda wasiya kutumikira Yehova? 5:10.
18. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Ma-
rco ndi Sidse? 19. Kodi ndinu wofunitsitsa kuchita chiyani?

KODI MUNGATSANZIRE BWANJI KULIMBA MTIMA KWA ZADOKI . . .

˛ pamene mukufuna kukhala- ˛ mukamathandiza abale ndi ˛ kuti mukhalebe okhulupirika


be kumbali ya Ufumu wa alongo anu? kwa Yehova?
Mulungu?

NYIMBO NA. 126


Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu
NKHANI
YOPHUNZIRA 28

Kodi Mumatha Kuzindikira


Choonadi?
NYIMBO NA. 123
Tizigonjera Mulungu “Khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi mchiuno
Mokhulupirika mwanu ngati lamba.”—AEF. 6:14.

ZIMENE TIPHUNZIRE ANTHU a Yehova amakonda choonadi chopezeka m’Mawu a


Tiona mmene tingadziphu- Mulungu. Zimene timawerenga m’mawu akewo zimalimbitsa
nzitsire kuti tizitha kusiya- chikhulupiriro chathu. (Aroma 10:17) Timakhulupirira kuti
nitsa pakati pa choonadi Yehova wakhazikitsa mpingo wa Chikhristu kuti ‘uzilimbikitsa
chimene Yehova watiphu- ndi kuteteza choonadi.’ (1 Tim. 3:15) Timasangalalanso kugo-
nzitsa ndi mfundo zabodza njera ‘amene akutsogolera’ pakati pathu akamafotokoza cho-
zimene Satana ndi otsutsa onadi cha m’Baibulo komanso kutipatsa malangizo ogwiriza-
amafalitsa. na ndi zimene Mulungu amafuna.—Aheb. 13:17.
2 Komabe, ngakhale kuti timadziwa choonadi komanso ku-

funika kotsatira malangizo a gulu la Mulungu, tikhoza kuso-


cheretsedwa. (Werengani Yakobo 5:19.) Satana amafuni-
tsitsa kuti tisiye kukhulupirira Baibulo komanso malangizo
amene timalandira kuchokera ku gulu la Mulungu.—Aef. 4:14.
3 Werengani Aefeso 6:13, 14. Posachedwapa, Mdyerekezi

adzagwiritsa ntchito mabodza pofuna kusokoneza anthu a mi-


tundu yonse kuti atsutsane ndi Yehova. (Chiv. 16:13, 14) Tiku-
dziwanso kuti Satana ayesetsa kwambiri kuti asokoneze anthu
a Yehova. (Chiv. 12:9) Choncho tingachite bwino kudziphu-
nzitsa kuti tizisiyanitsa choonadi ndi mfundo zabodza, n’ku-
mamvera choonadicho. (Aroma 6:17; 1 Pet. 1:22) Kuchita
1. Kodi timamva bwanji tikaganizira za choonadi chimene taphunzira?
2. Mogwirizana ndi Yakobo 5:19, kodi n’chiyani chingatichitikire pambuyo po-
phunzira choonadi?
3. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsitsa choonadi? (Aefeso 6:13, 14)

8
Kodi mukanakhulupirira ndani?
(Onani ndime 7)

zimenezi n’kumene kungathandize kuti tidza- tsa Yehova. (Miy. 2:3-6; Aheb. 5:14) Sitiyene-
pulumuke pa chisautso chachikulu. ra kulola kuti tiziopa kwambiri anthu kuposa
4 Munkhaniyi tikambirana makhalidwe awi- mmene timakondera Yehova chifukwa nthawi
ri amene angatithandize kuti tizizindiki- zambiri zimene anthu amakonda sizisangala-
ra choonadi chochokera m’Baibulo ndiponso tsa Mulungu.
kutsatira malangizo amene gulu la Mulungu 6 Tikamaopa kwambiri anthu kuposa Mulu-

limatipatsa. Kenako tikambirana zinthu zita- ngu tikhoza kupatutsidwa pa choonadi. Chi-
tu zimene tingachite kuti tigwiritsitse choo- tsanzo pa nkhaniyi ndi atsogoleri amafuko
nadi. 12 amene anapita kukaona dziko limene Mu-
MAKHALIDWE AMENE ANGATITHANDIZE lungu analonjeza kuti adzapereka kwa Aisi-
KUTI TIZIZINDIKIRA CHOONADI raeli. Atsogoleri 10 ankaopa kwambiri Aka-
5Kuopa Yehova. Kuopa Yehova moyenera nani kuposa mmene ankakondera Yehova.
kumatithandiza kuti tizimukonda kwambiri Iwo anauza Aisiraeli anzawo kuti: “Sitinga-
moti sitingachite chilichonse chimene chinga- the kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa
mukhumudwitse. Timafunitsitsa kuphunzira ndi amphamvu kuposa ifeyo.” (Num. 13:27-
kuti tizitha kusiyanitsa pakati pa zoyenera ndi 31) N’zoona kuti malinga n’kuona kwa anthu,
zosayenera ndiponso pakati pa choonadi ndi Akanani anali amphamvu kuposa Aisiraeli.
mfundo zabodza n’cholinga choti tizisangala- Koma ponena kuti Aisiraeli sakanatha ku-
gonjetsa adani awo ndiye kuti sankaganizira
4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
5. Kodi kuopa Yehova kumatithandiza bwanji kuzindikira 6. Kodi kuopa anthu kunachititsa bwanji atsogoleri 10 a
choonadi? Aisiraeli kupotoza choonadi?

JULY 2024 9
za Yehova. Atsogoleri 10 amenewa anafunika maganizo athu ndi anzeru kuposa mfundo za
kuganizira zimene Yehova ankafuna kuti Aisi- m’Malemba komanso malangizo amene gulu
raeli achite. Ankafunikanso kuganizira zime- la Yehova limatipatsa.
ne iye anali atangowachitira kumene. Ndiye- 9 Kuti tikhalebe odzichepetsa tiyenera ku-

no akanazindikira kuti mphamvu za Akanani kumbukira kuti ndife ang’ono kwambiri po-
zinali zochepa kwambiri poyerekezera ndi yerekezera ndi Yehova. (Sal. 8:3, 4) Tiye-
mphamvu za Yehova zopanda malire. Mosi- neranso kupemphera kuti tikhale ndi
yana ndi atsogoleri opanda chikhulupiriro- mtima wodzichepetsa komanso wophu-
wo, Yoswa ndi Kalebe ankafuna kusangalatsa nzitsika. Yehova adzatithandiza kuti tizi-
Yehova. Iwo anauza anthuwo kuti: “Nga- ona kuti maganizo ake, omwe timawaphu-
ti Yehova akusangalala nafe, adzatilowetsa- nzira kuchokera m’Baibulo komanso m’gulu
di mdzikolo nkulipereka kwa ife.”—Num. 14: lake, ndi ofunika kwambiri kuposa magani-
6-9. zo athu. Mukamawerenga Baibulo, muzipe-
7 Kuti tiziopa kwambiri Yehova, tiyenera ku- za umboni wotsimikizira kuti Yehova amako-
khala ofunitsitsa kuti tizimusangalatsa pa chi- nda anthu odzichepetsa osati onyada kapena
lichonse chomwe timasankha kuchita. (Sal. odzikuza. Tiyenera kuyesetsa kuti tikhale-
16:8) Mukamawerenga nkhani za m’Baibulo be odzichepetsa tikalandira utumiki umene
muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanakhala- umatichititsa kuti tizionekera kwambiri kwa
po, ndikanasankha kuchita chiyani?’ Mwachi- anthu.
tsanzo, yerekezerani kuti munkamva pamene ZIMENE TINGACHITE KUTI
atsogoleri amafuko 10 a Aisiraeli ankalankhu- TIGWIRITSITSE CHOONADI
la zinthu zosalimbikitsa. Kodi mukanakhu- 10 Muzikhulupirira malangizo ochokera ku-
lupirira zimene ankanena n’kuyamba kuopa gulu la Mulungu. Kale Yehova anagwiritsa
anthu, kapena kukonda kwanu Yehova kuka- ntchito Mose kenako Yoswa popereka mala-
nakuchititsani kuchita zinthu zomusangala- ngizo kwa Aisiraeli. (Yos. 1:16, 17) Aisirae-
tsa? Aisiraeli onse sanakhulupirire choonadi li ankadalitsidwa akamaona anthu amenewa
chimene Yoswa ndi Kalebe ankalankhula. Zo- ngati oimira Yehova Mulungu. Patapita zaka
tsatira zake n’zakuti onse anataya mwayi wo- zambiri, mpingo wa Chikhristu unakhazikitsi-
kalowa m’Dziko Lolonjezedwa.—Num. 14:10, dwa ndipo atumwi 12 ndi amene ankapere-
22, 23. ka malangizo. (Mac. 8:14, 15) Kenako m’gu-
8 Kudzichepetsa. Yehova amaulula choonadi lu la anthu opereka malangizowa munalinso
chake kwa anthu odzichepetsa. (Mat. 11:25) akulu a ku Yerusalemu. Chifukwa chotsatira
Ifeyo tinadzichepetsa n’kulola kuti tiphunzi- malangizo a amuna okhulupirikawa, “anthu
tsidwe choonadi. (Mac. 8:30, 31) Koma ti- m’mipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulu-
yenera kukhala osamala kuti tisayambe ku- piriro cholimba ndipo chiwerengero chinka-
dzikuza. Kunyada kungatichititse kuona kuti wonjezeka tsiku ndi tsiku.” (Mac. 16:4, 5)
Masiku anonso timadalitsidwa tikamatsatira
7. Kodi tingatani kuti tiziopa kwambiri Yehova? (Onani-
nso chithunzi.) 9. Kodi tingatani kuti tikhalebe odzichepetsa?
8. Kodi tiyenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe liti, ndi- 10. Kodi Yehova wakhala akugwiritsa ntchito ndani kuti
po n’chifukwa chiyani? apereke malangizo kwa anthu ake?

10 NSANJA YA OLONDA
Kodi mukanakhala kumbali ya ndani?
(Onani ndime 11)

malangizo ochokera kugulu la Yehova. Koma Ankafuna kuti akhale ndi mphamvu zambiri
kodi Yehova angamve bwanji ngati sitimvera komanso kutchuka. Mulungu anapha anthu
anthu amene iye wawasankha kuti azititsogo- amene ankatsogolera pa kuukirako komanso
lera? Tingapeze yankho la funsoli poganizira anthu masauzande ambiri amene anali ku-
zimene zinachitika pamene Aisiraeli ankapita mbali yawo. (Num. 16:30-35, 41, 49) Masi-
kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa. ku anonso, timadziwa kuti Yehova sasanga-
11 Pa nthawi ina Aisiraeli ali pa ulendo wo- lala ndi anthu amene salemekeza malangizo
kalowa m’Dziko Lolonjezedwa, amuna ena ochokera ku gulu lake.
12 Tiyenera kupitiriza kukhulupirira gulu la
otchuka ankatsutsa Mose komanso udindo
umene Yehova anamupatsa. Iwo ananena Yehova. Ngati pakufunika kusintha zime-
kuti: “Gulu lonseli [osati Mose yekha] ndi lo- ne timakhulupirira pa mfundo zina zake za
yera, ndipo Yehova ali pakati pawo.” (Num. m’Baibulo kapenanso njira imene timagwi-
16:1-3) N’zoona kuti Mulungu ankaona kuti rira ntchito za Ufumu, anthu amene amati-
‘gulu lonselo’ linali loyera, koma Yehova anali tsogolera sazengereza kusintha. (Miy. 4:18)
atasankha Mose kuti azitsogolera anthu ake. Iwo amachita zimenezi chifukwa amafunitsi-
(Num. 16:28) Potsutsana ndi Mose, anthu ou- tsa kusangalatsa Yehova. Iwo amayesetsanso
kirawa ankatsutsana ndi Yehova. M’malo mo- kusankha zochita pogwiritsa ntchito Mawu
ganizira zimene Yehova ankafuna, iwo anka- a Mulungu chifukwa m’Baibulo ndi momwe
ganizira kwambiri zimene iwowo ankafuna. muli mfundo zimene Akhristu onse amatsa-
tira.
11. Kodi n’chiyani chinachitikira Aisiraeli omwe sankale-
mekeza Mose amene Mulungu anamusankha kuti aziwa- 12. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira gulu la Ye-
tsogolera? (Onaninso chithunzi.) hova?

JULY 2024 11
Musamapusitsidwe ndi nkhani zabodza zomwe zingaoneke ngati zoona
(Onani ndime 15)

13 “Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olo- ulo anawaphunzitsa pa nthawi imene anali
ndola.” (2 Tim. 1:13) Mawu akuti “chitsanzo nawo limodzi. (2 Ates. 2:1-5) Iye analangi-
cha mawu olondola,” amatanthauza mfundo za abale akewo kuti asamangokhulupirira zi-
za m’Baibulo zimene Akhristu amakhulu- lizonse zimene amva. Pofuna kuwathandiza
pirira. (Yoh. 17:17) Chilichonse chimene ti- kuti izi zisadzawachitikirenso m’tsogolo, Pa-
makhulupirira chimachokera pa mfundo zi- ulo anamaliza kalata yake yachiwiri yopita
menezi. Gulu la Yehova latiphunzitsa kuti kwa Atesalonika ndi mawu akuti: “Landirani
tizigwiritsitsa mfundozi. Tikamachita zime- moni wanga, amene ineyo Paulo ndalemba
nezi tidzadalitsidwa. ndi dzanja langa. Nthawi zonse ndimalemba
14 Kodi n’chiyani chingachitike ngati tita-
chonchi mmakalata anga onse, kuti mudziwe
siya kutsatira “chitsanzo cha mawu olondo- kuti ndine amene ndalemba. Umu ndi mmene
la”? Taganizirani chitsanzo ichi. M’nthawi ya ndimalembera.”—2 Ates. 3:17.
atumwi Akhristu ena ankafalitsa mphekesera 15 Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a
yakuti tsiku la Yehova linali litafika. N’ku- Paulo opita kwa Atesalonika? Tikamva zi-
theka kuti panali kalata imene inanena zime- nazake zomwe sizikugwirizana ndi zomwe ti-
nezi ndipo anthu ankaganiza kuti inalembe-
maphunzira m’Baibulo kapenanso mpheke-
dwa ndi Paulo. Akhristu ena a ku Tesalonika
sera, tiyenera kuchita zinthu mwanzeru.
anayamba kukhulupirira komanso kufalitsa
M’dziko lomwe poyamba linkatchedwa Soviet
zimenezi asanafufuze. Iwo sakanapusitsidwa
Union, adani athu anafalitsa kalata yoone-
zikanakhala kuti anakumbukira zimene Pa-
ka ngati ikuchokera kulikulu lathu. Kalatayo
13. Kodi mawu akuti “chitsanzo cha mawu olondola” inalimbikitsa abale ena kuti apange kagu-
amatanthauza chiyani, nanga tiyenera kuchita chiyani
ndi mfundozi? 15. Kodi tingadziteteze bwanji ku nkhani zabodza zomwe
14. Kodi Akhristu ena anatani kuti asiye kutsatira “chi- zingaoneke ngati zoona? Perekani chitsanzo. (Onaninso
tsanzo cha mawu olondola”? zithunzi.)

12 NSANJA YA OLONDA
lu kena kapadera koima pakokha. Kalata- onadi, amayambitsa kuti anthu mumpingo
yo inkaoneka ngati yachokeradi kulikulu asamagwirizane, n’chifukwa chake Mulungu
lathu. Koma abale okhulupirika sanapusi- amatilangiza kuti ‘tiziwapewa.’ Kupanda ku-
tsidwe. Iwo anazindikira kuti uthenga wa tero tingapezeke kuti tapatutsidwa pa choo-
m’kalatayo sunkagwirizana ndi zomwe akhala nadi.—Werengani Aroma 16:17, 18.
akuphunzitsidwa. Masiku anonso adani athu 17 Tikazindikira choonadi komanso kuchi-

amagwiritsa ntchito njira zamakono pofuna gwiritsitsa, timakhala pa ubwenzi wabwino


kutisokoneza kapena kutichititsa kuti tisama- ndi Yehova komanso timakhala ndi chikhulu-
gwirizane. M’malo molola kuti wina aliyense piriro cholimba. (Aef. 4:15, 16) Sitimapusitsi-
“asinthe maganizo [athu]” omwe ndi olondo- dwa ndi mabodza komanso ziwembu za Sata-
la, tingadziteteze poganizira mosamala ngati na ndipo Yehova adzapitiriza kutiteteza pa
zimene tamva kapena kuwerenga zikugwiriza- chisautso chachikulu. Pitirizani kugwiritsitsa
na ndi mfundo za choonadi zomwe tikuzidzi- choonadi “ndipo Mulungu wamtendere adza-
wa kale.—2 Ates. 2:2; 1 Yoh. 4:1, khala nanu.”—Afil. 4:8, 9.
16 Pitirizani kugwirizana ndi anthu omwe ndi
17. Kodi kuzindikira komanso kugwiritsitsa choonadi ku-
okhulupirika kwa Yehova. Mulungu amafuna matithandiza bwanji?
kuti tizimulambira mogwirizana ndi abale ndi 
alongo athu. Tingapitirizebe kukhala ogwiri- MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI Tsamba 12: Chithu-
zana ngati tagwiritsitsa choonadi. Aliyense nzi choyerekezera chosonyeza pamene abale athu a
amene amachita zinthu zosemphana ndi cho- m’dziko lomwe linkatchedwa Soviet Union, analandira
kalata yooneka ngati yochokera kulikulu lathu koma ina-
16. Mogwirizana ndi Aroma 16:17, 18, kodi tiyenera ku- li yochokera kwa adani. Masiku ano adani athu angagwi-
chita chiyani ngati ena akuchita zinthu zosemphana ndi ritse ntchito intaneti pofalitsa nkhani zabodza zokhudza
choonadi? gulu la Yehova.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

˛ Kodi kuzindikira choonadi ˛ Kodi kuopa Yehova komanso ˛ Kodi n’chiyani chimene
n’kofunika bwanji? kudzichepetsa, kungatitha- chingatithandize kuti
ndize bwanji kuzindikira ko- tigwiritsitse choonadi?
manso kutsatira choonadi?

NYIMBO NA. 122


Khalani Olimba Komanso Osasunthika
NKHANI
YOPHUNZIRA 29

Tiyenera Kukhala Maso


Kuti Tizipewa Mayesero
NYIMBO NA. 121
Timafunika Kukhala “Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe
Odziletsa mmayesero.”—MAT. 26:41.

ZIMENE TIPHUNZIRE YESU ananena kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma
Nkhaniyi itithandiza kudzi- thupi ndi lofooka.”1 (Mat. 26:41b) Ponena zimenezi, iye
wa zimene tingachite kuti anasonyeza kuti ankamvetsa kuti anthufe si angwiro. Koma
tizipewa kuchita tchimo mawu akewanso ndi chenjezo loti tizipewa kudzidalira. Usiku
komanso zimene zingachi- womwewo asananene mawu amenewa, ophunzira ake anali
titse kuti tichite tchimolo. atasonyeza kudzidalira ponena kuti sadzasiya Mbuye wawo.
(Mat. 26:35) Iwo anali ndi zolinga zabwino koma sankadziwa
kuti sizikanakhala zophweka kuchita zimenezi ngati zinthu zi-
kanavuta kwambiri. Choncho Yesu anawachenjeza kuti: “Kha-
lani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mma-
yesero.”—Mat. 26:41a.
2 N’zomvetsa chisoni kuti ophunzirawo analephera kukhala

maso. Yesu atamangidwa, iwo anachita mantha ndipo anamu-


thawa. Chifukwa chakuti sanali maso ophunzirawo anachita
ndendende zomwe ananena kuti sangachite, zomwe ndi kumu-
siya Yesu.—Mat. 26:56.
3 Sitiyenera kudzidalira kwambiri kuti nthawi zonse tidza-

chita zoyenera. N’zoona kuti timafunitsitsa kuti tisachite


chilichonse chomwe chingakhumudwitse Yehova. Komabe si
ife angwiro choncho tikhoza kuyesedwa kuti tichite zoipa.
1 MATANTHAUZO A MAWU ENA: “Mzimu” wotchulidwa pa Mateyu 26:41, ndi mpha-
mvu yomwe imakhala mkati mwathu, imene imachititsa kuti tizimva kapena kuchita zi-
nthu m’njira inayake. Mawu akuti “thupi” akutanthauza kuti si ife angwiro. Choncho
tingakhale ndi zolinga zoyenera zoti tizichita zabwino, koma ngati sitingasamale tinga-
the kugonja tikayesedwa kuti tichite zimene Baibulo limanena kuti ndi zoipa.

1-2. (a) Kodi Yesu anawachenjeza chiyani ophunzira ake? (b) N’chifukwa chi-
yani ophunzirawo anamuthawa Yesu? (Onaninso zithunzi.)
3. (a) Kuti tipitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova, n’chifukwa chiyani tiye-
nera kupewa kudzidalira? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

14
Yesu anauza ophunzira ake kuti akhale maso n’cholinga choti
asayesedwe, koma iwo anamuthawa
(Onani ndime 1-2)

(Aroma 5:12; 7:21-23) Mosayembekezera, ti- ra zolaula. Pamene wina angamalimbane ndi
ngapezeke kuti tayamba kuona zinthu zi- vuto la kuopa anthu, kufuna kumangoyende-
nazake zoipa ngati zabwino. Kuti tikhalebe ra maganizo ake okha, kukwiya msanga ndi
okhulupirika kwa Yehova ndi Yesu, tiyene- zina. Monga mmene Yakobo ananenera, “mu-
ra kutsatira malangizo a Yesu oti tikhale- nthu aliyense amayesedwa ndi chilakolako
be maso. Nkhaniyi itithandiza kuti tizichita chake chimene chimamukopa ndi kumukola.”
zimenezi. Choyamba, tikambirana zinthu zi- —Yak. 1:14.
mene tiyenera kusamala nazo. Kenako tio- 6 Kodi mumadziwa zinthu zimene zingaku-
na zimene tingachite kuti tizipewa mayesero. yeseni inuyo mosavuta? Simuyenera kuma-
Pomaliza tikambirana zomwe zingatithandize dzinamiza n’kumanyalanyaza zofooka zanu
kuti tipitirize kukhala maso. kapena kumaganiza kuti ndinu wolimba kwa-
KODI TIYENERA KUKHALA mbiri moti simungachite zoipa. (1 Yoh. 1:8)
MASO PA ZINTHU ZITI? Ndipotu Paulo ananena kuti ngakhale anthu
4 Ngakhale machimo amene amaoneka “amene ndi oyenerera mwauzimu” akhoza ku-
ang’onoang’ono angathe kusokoneza ubwe- yesedwa ngati sangakhale maso. (Agal. 6:1)
nzi wathu ndi Yehova. Angachititsenso kuti Choncho tiyenera kukhala oona mtima n’ku-
tichite machimo akuluakulu. mazindikira zofooka zathu.—2 Akor. 13:5.
5 Tonsefe timayesedwa kuti tichite zoipa. 7 Kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindi-

Koma aliyense ali ndi zofooka zake, kaya zo- kira zinthu zimene zingachititse kuti tiyese-
mwe zingachititse kuti achite tchimo lalikulu, dwe mosavuta? Tizichita khama kuti tizipe-
ayambe kuchita makhalidwe oipa kapena ku- wa zinthu zimenezo. Mwachitsanzo, mizinda
gwera mumsampha woyamba kuganiza ngati yakale yomwe inkakhala ndi mipanda inka-
anthu a m’dzikoli. Wina angakhale ndi chila- tetezedwa kwambiri pageti chifukwa ndi pa-
kolako champhamvu chofuna kuchita zoipa mene adani akanadzera mosavuta kuti aukire.
monga kuseweretsa maliseche kapena kuone-
6. Kodi tiyenera kukhala oona mtima pa nkhani iti?
4-5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalanso maso ndi 7. Kodi tiyenera kudziwa bwino chiyani? Perekani chitsa-
machimo ang’onoang’ono? nzo.

JULY 2024 15
Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kudziwa zimene zinachitika, akhoza kupeza kuti pali
bwino zofooka zathu n’cholinga choti tizitha zina zomwe anachita mosaganiza bwino zo-
kupewa mayesero.—1 Akor. 9:27. mwe zachititsa kuti achite tchimolo. Zinthu
zimenezi zingaphatikizepo zosangalatsa zo-
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIPEWA MAYESERO
sayenera, kucheza ndi anthu a makhalidwe
8 Kodi tingatani kuti tizipewa mayesero? Ti- oipa kapena kupezeka m’malo okayikitsa,
yeni tione zimene tingaphunzire kwa wachi- kaya malo enieni kapena pa intaneti. N’kuthe-
nyamata wotchulidwa pa Miyambo chaputa- kanso kuti mwina anasiya kupemphera, kuwe-
la 7. Iye anagona ndi mkazi wachiwerewere. renga Baibulo, kupezeka pamisonkhano ka-
Vesi 22 limatiuza kuti “mwadzidzidzi,” wa- penanso kugwira ntchito yolalikira. Choncho
chinyamatayo anayamba kulondola mkaziyo. mofanana ndi wachinyamata wa m’buku la
Koma mavesi a m’mbuyo amasonyeza kuti iye Miyambo, tchimo lake silingakhale kuti lango-
anachitanso zinthu zina zomwe mwapang’o- chitika “mwadzidzidzi.”
nopang’ono zinamufikitsa poti achite tchimo. 11 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Sitiyenera
9 Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa
kungopewa tchimo, koma tiyeneranso kupe-
kuti achite tchimo? Choyamba, iye “ankadu- wa zinthu zimene zingachititse kuti tichite
tsa mumsewu pafupi ndi mphambano” yo- tchimolo. Solomo anamveketsa bwino mfu-
lowera kunyumba ya mkazi wachiwerewere- ndo imeneyi pomwe anafotokoza nkhani ya
yo. Kenako anayamba kulowera kunyumba wachinyamata ndi mkazi wachiwerewere. Po-
ya mkaziyo. (Werengani Miyambo 7:8, 9.) chenjeza za mkaziyo Solomo anati: “Musaso-
Iye atamuona mayiyo sanatembenuke n’ku- chere nkuyamba kuyenda mnjira zake.” (Miy.
bwerera. M’malomwake analola kuti mka- 7:25) Ananenanso kuti: “Ukhale kutali kwa-
ziyo amukise komanso anamumvetsera po- mbiri ndi iye. Usayandikire pakhomo la nyu-
mwe ankafotokoza kuti anakapereka nsembe mba yake.” (Miy. 5:3, 8) Choncho timapewa
zamgwirizano. Mwina ankamuuza zimenezi machimo poyesetsa kupewa zinthu zimene zi-
pofuna kumuchititsa mnyamatayo kuti azi- ngachititse kuti tichite machimowo.1 Izi ziku-
muona kuti iye si munthu woipa. (Werenga- phatikizapo kupewa zinthu zimene si zolakwi-
ni Miyambo 7:13, 14, 21.) Wachinyamata- ka kwenikweni kwa Akhristu koma zikhoza
yo akanapewa zinthu zimenezi akanatetezeka kuchititsa kuti tiyesedwe.—Mat. 5:29, 30.
ndipo sakanachita tchimo. 12 Tiyenera kukhala otsimikiza mumtima

10 Nkhani imene Solomo analembayi ikuso- mwathu kuti tipewe zinthu zomwe zinga-
nyeza zimene zingachitikire mtumiki wa Ye- tichimwitse. Izi ndi zimene Yobu anachita.
hova aliyense. Iye angathe kuchita tchimo 1 Munthu amene wachita tchimo lalikulu angapeze mfundo zo-
lalikulu n’kumaona kuti zachitika “mwadzi- thandiza m’buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale,
dzidzi.” Kapenanso angathe kunena kuti “za- phunziro 57 mfundo 1-3 komanso mu nkhani yakuti “Maso Ako
Aziyang’ana pa Zinthu Zakutsogolo” mu Nsanja ya Olonda ya
ngochitika.” Koma ataganizira bwinobwino November 2020, tsamba 27-29, ndime 12-17.

8-9. Kodi wachinyamata wotchulidwa pa Miyambo cha- 11. Kodi tiyenera kupewa zinthu ziti kuti tisachite
putala 7 akanatani kuti apewe kuchita tchimo? (Miyambo tchimo?
7:8, 9, 13, 14, 21) 12. Kodi Yobu anatsimikiza mtima kuchita chiyani, na-
10. Kodi masiku ano munthu angachite bwanji zinthu nga zimenezi zinamuthandiza bwanji kuti asayesedwe?
ngati wachinyamata wotchulidwa m’buku la Miyambo? (Yobu 31:1)

16 NSANJA YA OLONDA
Iye ‘anachita pangano ndi maso ake’ kuti tchimo lalikulu.—Afil. 4:8; Akol. 3:2; Yak. 1:
asayang’ane akazi ena mowasirira. (We- 13-15.
rengani Yobu 31:1.) Kuchita zinthu mo- 14 Kodi n’chiyaninso chingatithandize kuti

gwirizana ndi panganolo kunamuthandiza tipewe mayesero? Tiyenera kutsimikizira kuti


kuti asachite chigololo. Ifenso tiyenera kupe- nthawi zonse kumvera malamulo a Yehova
wa chilichonse chomwe chingachititse kuti ti- n’kothandiza. N’zoona kuti nthawi zina ti-
yesedwe. khoza kuvutika kuti maganizo athu komanso
13 Tiyeneranso kuteteza maganizo athu.
zimene timalakalaka zigwirizane ndi zomwe
(Eks. 20:17) Ena amaganiza kuti si kulakwa Yehova amafuna. Koma tikayesetsa kutero ti-
kuganizira zinthu zoipa bola ngati sakuchi- makhala ndi mtendere mumtima.
ta zinthuzo. Koma maganizo amenewa ndi 15 Tiyenera kuyesetsa kuti tizilakalaka zi-
olakwika. Munthu amene amaganizira kwa- nthu zoyenera. Tikaphunzira ‘kudana ndi
mbiri zinthu zolakwika amayamba kuzilakala- choipa n’kumakonda chabwino’ tidzatsimiki-
ka kwambiri. Akamachita zimenezi zimakhala za mtima kuti tizichita zoyenera n’kumape-
zovuta kuti apewe mayesero. N’zoona kuti wa zinthu zimene zingachititse kuti tichimwe.
nthawi zina tikhoza kuyamba kuganizira zi- (Amosi 5:15) Kulakalaka zinthu zoyenera ku-
nthu zolakwika. Koma chofunika ndi kusi- dzatithandiza kuti tisatengeke tikakumana
ya kuganizira zimenezo n’kuyamba kuganizi- ndi mayesero amene sitimayembekezera ka-
ra zinthu zabwino. Tikatero maganizo oipawo penanso ovuta kuwapewa.
sakula n’kufika pokhala chilakolako cha-
mphamvu chomwe chingachititse kuti tichite 14. Kodi n’chiyaninso chingatithandize kuti tipewe maye-
sero?
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza maganizo 15. Kodi kulakalaka zinthu zoyenera kungatithandize
athu? (Onaninso zithunzi.) bwanji kupewa mayesero?

Tiyenera kupewa chilichonse chomwe chingachititse kuti tiyesedwe


(Onani ndime 13)

JULY 2024 17
Kuchita zinthu zimene zingatichititse kukhala pa ubwenzi ndi Yehova nthawi zonse kungatithandize kuti tipewe mayesero
(Onani ndime 16)

16Kodi tingatani kuti tizilakalaka zinthu zo- nkhaniyi ndi mtumwi Petulo. Chifukwa cho-
yenera? Tiyenera kumatanganidwa ndi zi- opa anthu iye anakana Yesu katatu. (Mat.
nthu zokhudza kulambira. Tikakhala pamiso- 26:69-75) Koma pamene analankhula moli-
nkhano kapena mu utumiki zimakhala zovuta mba mtima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayu-
kuti tiyesedwe. M’malomwake timalimbikitsi- da, zinkaoneka ngati anasiya kuchita mantha.
dwa kukhala ndi mtima wofuna kusangala- (Mac. 5:27-29) Koma pa nthawi ina patapita
tsa Yehova. (Mat. 28:19, 20; Aheb. 10:24, 25) zaka zingapo, iye anasiya kudya ndi Akhristu
Tikamawerenga, kuphunzira komanso kuga- a mitundu ina “chifukwa ankaopa anthu odu-
nizira mozama Mawu a Mulungu timayamba lidwawo.” (Agal. 2:11, 12) Apa tingati anaya-
kukonda zabwino ndipo timadana ndi zo- mbiranso kuopa anthu. N’kutheka kuti vuto
ipa. (Yos. 1:8; Sal. 1:2, 3; 119:97, 101) Ku- lake la manthali linali lisanatheretu.
mbukirani kuti Yesu anauza ophunzira ake 18 Mofanana ndi Petulo, mwina ifenso ti-
kuti: “Mupitirize kupemphera kuti musalowe ngamalimbane ndi vuto linalake mobwere-
mmayesero.” (Mat. 26:41) Tikamapemphera zabwereza, lomwe tinkaganiza kuti tinatha-
kwa Atate wathu wakumwamba, iye amatitha- na nalo. Mwachitsanzo, m’bale wina ananena
ndiza ndipo ifeyo timafunitsitsa kumusanga- kuti: “Ndinasiya kuonera zolaula kwa zaka
latsa.—Yak. 4:8. 10, ndipo ndinkaganiza kuti basi vutoli nda-
PITIRIZANI KUKHALA MASO thana nalo. Koma vutoli linangobisala n’ku-
Anthufe tikhoza kusiyiratu makhalidwe
17 mayembekezera nthawi yoti lionekerenso.”
ena oipa. Koma tikhoza kumavutikabe ndi N’zosangalatsa kuti m’baleyu sanagonje. Iye
mtima wofuna kuchita zoipa. Chitsanzo pa anaona kuti anafunika kuchita khama tsiku
lililonse kuti azilimbana ndi vutoli, mwina-
16. Kodi kutanganidwa ndi zinthu zokhudza kulambira nso kwa moyo wake wonse m’dziko loipali.
kungatiteteze bwanji? (Onaninso zithunzi.)
17. Kodi Petulo ankalimbana ndi vuto liti mobwerezabwe- 18. Kodi n’chiyani chomwe chingachitike ndi makhalidwe
reza? ena oipa omwe tingakhale nawo?

18 NSANJA YA OLONDA
Mothandizidwa ndi mkazi wake komanso aku- Yehova kumachititsa kuti munthu akhale wo-
lu, iye anachita zonse zomwe akanatha kuti sangalala kwambiri. (Aheb. 11:25; Sal. 19:8)
azipewa kuonera zolaula. Zili choncho chifukwa chakuti anthufe ti-
19 Kodi tingatani kuti vuto lomwe sitina- nalengedwa m’njira yoti tizitsatira mfundo
thane nalo lisatichimwitse? Chomwe chinga- za Mulungu. (Gen. 1:27) Tikamachita zime-
tithandize ndi kutsatira malangizo a Yesu nezi, timakhala ndi chikumbumtima choye-
pa nkhani ya mayesero. Iye anati: “Khala- ra komanso timayembekezera moyo wosatha.
ni maso.” Ngakhale pa nthawi imene mukuo- —1 Tim. 6:12; 2 Tim. 1:3; Yuda 20, 21.
na kuti ndinu olimba mwauzimu, muzipitiriza 21 N’zoona kuti “thupi ndi lofooka.” Koma

kupewa zinthu zimene zingachititse kuti mu- sizikutanthauza kuti tilibiretu mtengo wogwi-
lowe m’mayesero. (1 Akor. 10:12) Muzipitiriza ra. Yehova ndi wokonzeka kutipatsa mpha-
kuchita zinthu zimene zinakuthandizani kuti mvu. (Werengani 2 Akorinto 4:7.) Onani
mugonjetse vutolo. Lemba la Miyambo 28:14 kuti Mulungu amapereka mphamvu yoposa
limati: “Wosangalala ndi munthu amene ntha- yachibadwa. Koma choyamba, tiyenera ku-
wi zonse amasamala zochita zake.”—2 Pet. gwiritsa ntchito mphamvu yathu yachibadwa
3:14. polimbana ndi mayesero tsiku lililonse. Tika-
chita mbali yathu tisamakayikire kuti Yeho-
MADALITSO AMENE TINGAPEZE
va adzayankha mapemphero athu potipatsa
CHIFUKWA CHOKHALABE MASO
mphamvu zowonjezereka zomwe tingafuniki-
20 Tisamakayikire kuti kukhalabe maso re. (1 Akor. 10:13) Choncho mothandizidwa
n’kothandiza nthawi zonse. Machimo ama- ndi Yehova tikhoza kukhala maso n’kumape-
ngochititsa kuti munthu ‘asangalale kwa wa mayesero.
nthawi yochepa’ koma kutsatira mfundo za
19. Kodi tingatani ngati tili ndi vuto limene sitinaligonje-
tsebe? 

20-21. (a) Kodi ndi madalitso ati omwe tingapeze tika- MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI Tsamba 18: M’bale
makhala maso kuti tipewe mayesero? (b) Ngati ife tita- akuwerenga lemba la tsiku m’mawa, akuwerenga Baibulo
chita mbali yathu, kodi Yehova adzatithandiza bwanji? pa nthawi yopuma masana, ndipo madzulo wapezeka
(2 Akorinto 4:7) pamisonkhano.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

˛ Kodi tiyenera kukhala maso ˛ Kodi tingatani kuti tikhale ˛ N’chifukwa chiyani tiyenera
pa zinthu ziti kuti tipewe ma- maso n’kumapewa maye- kupitiriza kukhala maso?
yesero? sero?

NYIMBO NA. 47
Muzipemphera kwa Yehova Tsiku Lililonse
NKHANI
YOPHUNZIRA 30

Zimene Tikuphunzira
kwa Mafumu a Chiisiraeli
“Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa
NYIMBO NA. 36 ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi
Timateteza Mtima Wathu amene sakumutumikira.”—MAL. 3:18.

ZIMENE TIPHUNZIRE BAIBULO limatiuza za amuna 40 omwe anakhala mafumu a Isi-


Kuona zomwe Yehova raeli.1 Limafotokoza mosapita m’mbali zimene ena mwa mafu-
ankayang’ana mwa mafu- muwa anachita. Mwachitsanzo ngakhale mafumu ena abwino
mu a Chiisiraeli kutithandi- anachitanso zinthu zina zoipa. Chitsanzo ndi Davide yemwe ana-
za kuona zimene iye ama- li mfumu yabwino. Yehova ananena kuti: “Davide mtumiki wa-
funa kuti atumiki ake nga. . . anasunga malamulo anga, kunditsatira ndi mtima wake
azichita masiku ano. wonse ndiponso kuchita zinthu zoyenera zokhazokha pamaso
panga.” (1 Maf. 14:8) Komatu munthu ameneyu anachita chigo-
lolo ndi mkazi wa mwiniwake ndipo anakonza zoti mwamuna wa
mkaziyo aphedwe kunkhondo.—2 Sam. 11:4, 14, 15.
2 Baibulo limatiuzanso za mafumu ambiri osakhulupirika

omwe anachitanso zinthu zina zabwino. Chitsanzo ndi Mfumu


Rehobowamu. Kwa Yehova “iye anachita zoipa.” (2 Mbiri 12:14)
Koma Rehobowamu anamvera lamulo la Mulungu loti alole kuti
ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli ukhale woima paokha. Anachita-
nso zinthu zothandiza mtundu wake pomanga mizinda yokhala
ndi mipanda yolimba kwambiri.—1 Maf. 12:21-24; 2 Mbiri 11:
5-12.
3 Funso lofunika kwambiri ndi lakuti: Ngati mafumu a Chiisira-

eli ankachita zabwino ndi zoipa, n’chiyani chinkachititsa Yeho-


va kuona mafumu ena kukhala okhulupirika? Yankho la funso
1 Munkhaniyi, mawu akuti “mafumu a Isiraeli” akunena za mafumu onse omwe anala-
mulira anthu a Yehova, kaya mu ufumu wa Yuda wa mafuko awiri kapena wa Isiraeli wa
mafuko 10, kapenanso omwe analamulira mafuko onse 12.

1-2. Kodi Baibulo limatiuza zinthu ziti zokhudza mafumu ena a Isiraeli?
3. Kodi ndi funso lofunika liti lomwe tiyenera kuliganizira, nanga tikambirana
chiyani munkhaniyi?

20
limeneli litithandiza kudziwa zimene Yehova pirika n’kupitiriza kutumikira Yehova ndi mti-
amafuna kuti ifeyo tizichita. Tikambirana zi- ma wonse? Tingachite zimenezi popewa zinthu
nthu zitatu zimene iye ankayang’ana mwa ma- zimene zingachititse kuti tikhale osakhulu-
fumu a Chiisiraeli. Iye ankayang’ana mtima pirika. Mwachitsanzo, zosangalatsa zosayene-
wawo, kulapa kwawo komanso zimene ankachi- ra, kugwirizana ndi anthu oipa komanso ku-
ta popitirizabe kumulambira m’njira yolondola. konda chuma zingachititse kuti tisamatumikire
ANKATUMIKIRA YEHOVA NDI MTIMA WONSE
Mulungu ndi mtima wonse. Tikazindikira kuti
pali zinazake zomwe zikuchititsa kuti chikondi
4 Mafumu omwe Yehova anasangalala nawo
chathu kwa Yehova chiyambe kuchepa, tizichi-
ankamutumikira ndi mtima wonse.1 Mwachitsa-
tapo kanthu mwamsanga.—Werengani Miya-
nzo, Yehosafati yemwe anali mfumu yabwino,
mbo 4:23; Mateyu 5:29, 30.
“anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” 7 Tisamalole kuti mtima wathu ukhale wo-
(2 Mbiri 22:9) Pofotokoza za Yosiya, Baibulo li-
gawanika. Ngati sitingasamale tikhoza ku-
mati: “Iye asanakhale mfumu, panalibe mfumu
ina imene inabwerera kwa Yehova ndi mtima madzinamiza n’kumaona kuti ngati tikuchita
wake wonse.” (2 Maf. 23:25) Nanga bwanji za zambiri potumikira Yehova, palibe chimene chi-
Solomo yemwe pamapeto pake anachita zoipa? ngachititse kuti tichite zoipa. Tiyerekeze kuti
Baibulo limati: “Sanatumikire Yehova Mulungu kunja kuli chimphepo komanso fumbi. Ndiye
wake ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 11:4) Ndi- inu mwakonza bwinobwino m’nyumba mwanu.
po ponena za Abiyamu, yemwenso anali mfumu Kodi mungasiye mawindo ndi zitseko zili zo-
yosakhulupirika, Baibulo limati: “Sanatumiki- tsegula kuti fumbi lizilowa m’nyumbamo? Ayi.
re Yehova Mulungu wake ndi mtima wonse.” Mfundo yake ndi yakuti timafunika kuchita za-
—1 Maf. 15:3. mbiri osati kungodya chakudya chauzimu cho-
5 Ndiye kodi kutumikira Yehova ndi mtima mwe chimatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi
wonse kumatanthauza chiyani? Munthu amene wabwino ndi Yehova. Tiyeneranso kutseka chi-
amatumikira Mulungu ndi mtima wake wonse tseko, kunena kwake titero, kuti fumbi la m’dzi-
samangomulambira chifukwa chakuti ndi zi- koli kapena zinthu zimene Mulungu amadana
mene akuyenera kuchita. M’malomwake, ama- nazo zisalowe mumtima mwathu n’kuugawani-
mutumikira chifukwa cha chikondi komanso tsa.—Aef. 2:2.
mtima wodzipereka. Kuwonjezera pamenepo, ANALAPA MACHIMO AWO
amapitiriza kumukonda komanso kudzipereka 8 Monga taonera kale, Mfumu Davide inachi-
kwa iye kwa moyo wake wonse.
6 Kodi tingatsanzire bwanji mafumu okhulu-
ta tchimo lalikulu. Koma mneneri Natani ata-
mudzudzula chifukwa cha tchimo lakelo, Da-
1 TANTHAUZO LA MAWU ENA: Nthawi zambiri Baibulo limagwi- vide anadzichepetsa n’kulapa. (2 Sam. 12:13)
ritsa ntchito mawu akuti “mtima” pofotokoza mmene munthu Mawu ake opezeka mu Salimo 51 akusonyeza
alili, zomwe zikuphatikizapo zimene amalakalaka, zimene ama-
ganiza, khalidwe lake, luso, komanso zolinga zake. kuti iye analapadi mochokera pansi pa mtima.
Sikuti Davide anangoyerekezera kudzimvera
4. Kodi panali kusiyana kotani pakati pa mafumu okhu-
lupirika ndi mafumu osakhulupirika? 7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa zinthu zimene zi-
5. Fotokozani zimene kutumikira Yehova ndi mtima wo- ngachititse kuti tisiye kukonda Mulungu?
nse kumatanthauza. 8-9. Kodi Mfumu Davide ndi Mfumu Hezekiya anachita
6. Kodi tingatani kuti tipitirize kutumikira Mulungu ndi bwanji atadzudzulidwa? (Onaninso chithunzi chapachi-
mtima wonse? (Miyambo 4:23; Mateyu 5:29, 30) kuto.)

JULY 2024 21
chisoni pofuna kupusitsa Natani kapena kuze- ngizo komanso kudzudzulidwa. (Aheb. 12:6)
mba kulandira chilango.—Sal. 51:3, 4, 17, tima- Choncho tikamapatsidwa malangizo, tiyenera
wu tapamwamba. (1) kuwalandira modzichepetsa, (2) kusintha
9 Mfumu Hezekiya nayonso inachimwira Ye- pamene pakufunika kutero, komanso (3) kupi-
hova. Baibulo limati: “Mtima wake unayamba tiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse. Ti-
kudzikuza ndipo zimenezi zinachititsa kuti Mu- kalapa machimo athu Yehova adzatikhululuki-
lungu amukwiyire iyeyo, Yuda ndiponso Yeru- ra.—Werengani 2 Akorinto 7:9, 11.
salemu.” (2 Mbiri 32:25) N’chifukwa chiyani ANKALAMBIRA YEHOVA M’NJIRA YOYENERA
Hezekiya anayamba kunyada? N’kutheka kuti 12 Yehova ankaona kuti mafumu omwe anka-
iye ankadziona kuti ndi wapamwamba chifukwa
mulambira m’njira yoyenera ndi okhulupiri-
cha chuma chake, kupambana kwake pankho-
ka. Mafumuwo ankalimbikitsanso anthu awo
ndo yolimbana ndi Asuri, kapenanso kuchiritsi-
kuti azichita zomwezo. Monga taonera, n’zoo-
dwa kwake modabwitsa. N’kutheka kuti kunali
na kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina. Koma iwo
kunyada komwe kunamuchititsa kuti aonetse
ankalambira Yehova yekha ndipo ankayesetsa
Ababulo chuma chake ndipo mneneri Yesaya
kuwononga mafano m’dzikolo.1
anamudzudzula. (2 Maf. 20:12-18) Koma mo- 13 N’chifukwa chiyani Yehova anaweruza ma-
fanana ndi Davide, Hezekiya anadzichepetsa
fumu ena kuti anali osakhulupirika? Sikuti zo-
n’kulapa. (2 Mbiri 32:26) Zotsatira zake n’zaku-
nse zimene mafumuwa ankachita zinali zoipa.
ti Yehova ankamuona monga mfumu yokhu-
Ngakhale Ahabu yemwe anali mfumu yoipa ana-
lupirika yomwe ‘inkachita zoyenera.’—2 Maf.
dzichepetsa komanso kukhudzidwa chifukwa
18:3.
10 Mosiyana ndi Davide ndi Hezekiya, Mfumu
chochititsa kuti Naboti aphedwe. (1 Maf. 21:
27-29) Iye anamanganso mizinda ndipo anapa-
Amaziya ya ku Yuda anachita zoyenera “koma mbana nkhondo zambiri ku Isiraeli. (1 Maf. 20:
osati ndi mtima wonse.” (2 Mbiri 25:2) Kodi 21, 29; 22:39) Koma Ahabu anachita zoipa kwa-
analakwitsa pati? Yehova atamuthandiza kugo- mbiri pomwe anamvera mkazi wake n’kumali-
njetsa Aedomu, Amaziya anayamba kulambi- mbikitsa Aisiraeli kuti azilambira mafano. Ata-
ra Milungu yawo.1 Ndiye mneneri wa Yehova chita zimenezi iye sanalape.—1 Maf. 21:25, 26.
atabwera kudzamudzudzula, Amaziya anachita 14 Chitsanzo chinanso cha mfumu yosakhulu-
makani n’kumuthamangitsa.—2 Mbiri 25:14-16.
pirika ndi Rehobowamu. Monga taonera kale,
11 Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzozi?

Tiyenera kulapa machimo athu n’kuyesetsa kuti 1 Mfumu Asa anachita machimo aakulu. (2 Mbiri 16:7, 10) Koma
Baibulo limasonyeza kuti Yehova ankamuona kuti anachita za-
tisawabwerezenso. Nanga kodi tizitani akulu bwino. Ngakhale kuti poyamba anakana atadzudzulidwa, n’ku-
akatipatsa malangizo pa zinthu zooneka ngati theka kuti pambuyo pake analapa. Koma zabwino zimene ana-
zazing’ono? Tisamaone ngati akuluwo komanso chita ndi zambiri tikayerekezera ndi zimene analakwitsa.
Chofunika kwambiri ndi chakuti Asa ankalambira Yehova yekha
Yehova satikonda. Ngakhale mafumu abwino ndipo anayesetsa kuchotsa mafano mu ufumu wake.—1 Maf.
a ku Isiraeli ankafunikanso kupatsidwa mala- 15:11-13; 2 Mbiri 14:2-5.

1 Zikuoneka kuti nthawi zambiri, mafumu achikunja ankalambi- 12. Kodi mafumu okhulupirika ankasiyana bwanji ndi
ra milungu ya mitundu imene aigonjetsa. mafumu osakhulupirika?
13. N’chifukwa chiyani Yehova anaweruza kuti Ahabu
10. Kodi Mfumu Amaziya anatani atadzudzulidwa? anali wosakhulupirika?
11. Mogwirizana ndi 2 Akorinto 7:9, 11, kodi tiyenera ku- 14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ankaona kuti Reho-
chita chiyani kuti Yehova atikhululukire? (Onaninso zithu- bowamu anali mfumu yosakhulupirika? (b) Kodi n’chiya-
nzi.) ni chomwe chinkachitika mu ulamuliro wa mafumu oipa?

22 NSANJA YA OLONDA
Tikapatsidwa malangizo, tiyenera (1) kuwalandira modzichepetsa, (2) kusintha, komanso
(3) kupitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse
(Onani ndime 11)

mu ulamuliro wake iye anachita zinthu zina za- mbiri? Chifukwa chimodzi n’chakuti mafumu-
bwino. Koma ufumu wake utakhala wampha- wa anali ndi udindo waukulu wotsogolera anthu
mvu iye anasiya kutsatira Chilamulo cha Yeho- a Mulungu kuti azimulambira m’njira yoyenera.
va n’kuyamba kulambira mafano. (2 Mbiri 12:1) Komanso kulambira mafano kumachititsa kuti
Choncho ankalambira Yehova kwinaku n’kuma- ena azichita machimo akuluakulu komanso zo-
lambira milungu yabodza. (1 Maf. 14:21-24) Re- panda chilungamo. (Hos. 4:1, 2) Kuwonjezera
hobowamu ndi Ahabu si mafumu okhawo ame- pamenepo, mafumuwo komanso anthuwo anali
ne anasiya kulambira Yehova m’njira yoyenera. mtundu wodzipereka kwa Yehova. N’chifukwa
Ndipotu mafumu ambiri osakhulupirika ankala- chake Baibulo limayerekezera kulambira kwa-
mbira mafano komanso kulimbikitsa ena kuti wo mafano ndi chigololo. (Yer. 3:8, 9) Munthu
azichita zomwezo. Choncho n’zoonekeratu kuti amene wachita chigololo amakhala kuti wala-
kulambira Yehova m’njira yoyenera ndi chifu- kwira kwambiri mwamuna kapena mkazi wake.
kwa chachikulu chomwe chinkachititsa Yehova Mofanana ndi zimenezi mtumiki wodzipereka
kuti aziona mfumu kukhala yabwino kapena yo- wa Yehova yemwe amalambira mafano amakha-
ipa. la kuti wamulakwira kwambiri Yehova.1—Deut.
15 N’chifukwa chiyani Yehova ankaona kuti 4:23, 24.
nkhani yokhudza kulambira ndi yofunika kwa- 1 Tikudziwa kuti nkhani ya kulambira ndi yofunika kwambiri kwa
Yehova chifukwa chakuti malamulo awiri oyamba mu Chilamu-
15. N’chifukwa chiyani kulambira m’njira yoyenera kuli lo cha Mose ankaletsa kulambira munthu kapena chinthu chili-
kofunika kwa Yehova? chonse koma Yehova yekha.—Eks. 20:1-6.

JULY 2024 23
16 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera ku-
yesetsa kuti tizipewa kulambira milungu ya-
bodza. Koma tiyeneranso kupitiriza kulambira
Yehova m’njira yoyenera n’kumachita zambi-
ri pomutumikira. Mneneri Malaki anafoto-
Mukhoza Kubwerera
koza momveka bwino zimene zimachititsa kwa Yehova
Yehova kuona kuti munthu ndi wabwino kape-
na woipa. Iye analemba kuti: “Mudzaona- Taganizirani za Mfumu Manase yemwe “ana-
nso kusiyana pakati pa munthu wolungama chita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yeho-
ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene va.” Iye “anaphanso anthu ambiri osalakwa,”
akutumikira Mulungu ndi amene sakumutu- ankachita zamatsenga komanso anafika po-
pereka ana ake monga nsembe kwa milungu
mikira.” (Mal. 3:18) Choncho sitiyenera kulo-
yabodza. (2 Maf. 21:6, 16) Iye anachititsa
la chilichonse, kaya zofooka zathu kapena
Ayuda kuchita “zinthu zoipa kuposa zimene
zimene timalakwitsa, kuti zitikhumudwitse
mitundu” ina inkachita. (2 Maf. 21:9; 2 Mbiri
mpaka kufika posiya kutumikira Mulungu. Kusi- 33:1-6) Koma Manase atatengedwa kukakha-
ya kutumikira Yehova pakokha ndi tchimo lali- la kapolo ku Babulo, analapa. Ayenera kuti
kulu. anapempha maulendo angapo kuti akhululu-
17 Ngati mukuganizira zolowa m’banja, mawu kidwe. Paja iye anachita machimo akuluakulu
omwe Malaki ananena okhudza kutumikira Mu- kwa nthawi yaitali. Manase anapitiriza ‘ku-
lungu angakuthandizeni kusankha bwino wo- dzichepetsa komanso anapitiriza ‘kupe-
kwatirana naye. Munthu akhoza kukhala ndi mphera’ kwa Mulungu. Kodi zotsatira zake
makhalidwe ena abwino. Koma ngati saku- zinali zotani? Yehova “anamva pemphero lake
tumikira Mulungu woona, kodi Yehova akhoza lochonderera” ndipo anamuyankha. Iye ana-
kumuona ngati munthu wolungama? (2 Akor. mukhululukira ndipo anamubwezeretsa pa
ufumu wake ku Yerusalemu.—2 Mbiri 33:
6:14) Ngati mutakhala naye m’banja, kodi anga-
12, 13.
kulimbikitseni pa nkhani yotumikira Mulungu?
Taganizirani izi: N’kutheka kuti akazi achiku- Kodi Yehova angakhululukirenso anthu ame-
nja a Solomo anali ndi makhalidwe ena abwi- ne anasiya kumutumikira, omwe alapa kucho-
kera pansi pa mtima? Inde, chifukwa lemba la
no. Koma popeza kuti sankatumikira Yeho-
Yesaya 55:7 limati: “Munthu woipa asiye njira
va, pang’ono ndi pang’ono anapatutsa mtima
yake ndipo wopweteka anzake asiye magani-
wake moti anayamba kulambira milungu yabo-
zo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adza-
dza.—1 Maf. 11:1, 4. muchitira chifundo. Abwerere kwa Mulungu
18 Makolo, mungathe kugwiritsa ntchito nkha-
wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mti-
ni zokhudza mafumu otchulidwa m’Baibu- ma wonse.” Choncho yesetsani kuchita zo-
lo pothandiza ana anu kuti azitumikira Ye- nse zomwe mungathe kuti mubwerere kwa
hova ndi mtima wawo wonse. Muziwathandiza Yehova.

16. Kodi n’chiyani chimachititsa Yehova kuona kuti mu-


nthu ndi wolungama kapena woipa?
17. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha wo-
kwatirana naye?
18. Kodi makolo ayenera kuphunzitsa chiyani ana awo?

24 NSANJA YA OLONDA
kudziwa kuti Yehova ankaona mfumu kukha- pindula chifukwa amayambiranso kukhala pa
la yabwino kapena yoipa malinga ndi zime- ubwenzi ndi Yehova.
ne inkachita polimbikitsa kulambira koona. 20 Ndiye kodi taphunzira chiyani kuchoke-

Zolankhula komanso zochita zanu zizisonye- ra kwa mafumu a Chiisiraeli? Tikhoza ku-
za kuti zinthu zokhudza kulambira monga khala ngati mafumu okhulupirika ngati tita-
kuphunzira Baibulo, kupezeka pamisonkhano pitiriza kutumikira Yehova ndi mtima wonse.
komanso kugwira ntchito yolalikira ndi zofuni- Tiziphunzira pa zimene talakwitsa, kulapa ko-
ka kwambiri kuposa chilichonse. (Mat. 6:33) manso kusintha. Tizikumbukiranso kufunika
Kupanda kutero, anawo akhoza kumangoona kolambira Mulungu woona yekha. Mukapitiriza
ngati ndi a Mboni za Yehova chifukwa cha- kukhala okhulupirika kwa Yehova iye adzakuo-
kuti akungotsatira makolo awo. Zotsatira zake nani inuyo monga munthu amene amachita zo-
n’zakuti sangamaike pamalo oyamba kulambira yenera.
koona mwinanso kungosiyiratu kulambira Ye- 20. Kodi Yehova adzationa bwanji tikamatsanzira mafu-
hova. mu okhulupirika?
19 Kodi munthu amene wasiya kutumikira Ye-

hova sangadzakhalenso naye pa ubwenzi? Ayi,


chifukwa akhoza kulapa n’kuyambiranso kumu-
lambira m’njira yoyenera. Kuti zimenezi zithe- 
ke, ayenera kudzichepetsa n’kulola kuti atha- MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI Pachikuto: Mfumu Da-
ndizidwe ndi akulu. (Yak. 5:14) N’zoona kuti vide komanso Mfumu Hezekiya anadzichepetsa n’kulapa
angafunike kuchita khama, koma khamalo lima- atadzudzulidwa chifukwa cha machimo awo. Tsamba 23:
Mkulu wachinyamata akupereka malangizo kwa m’bale
19. Kodi pali mwayi wotani kwa amene anasiya kutumiki- wina pa nkhani yokhudza mowa. M’baleyo wavomera
ra Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “Mukhoza Kubwerera malangizowo modzichepetsa, wasintha ndipo akupitiriza
kwa Yehova.”) kutumikira Yehova mokhulupirika.

KODI TINGATANI KUTI . . .

˛ tizitumikira Yehova ndi ˛ tisonyeze kuti talapa? ˛ tizilambira Mulungu m’njira


mtima wonse? yoyenera?

NYIMBO NA. 45
Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga
Kodi Mungatani Kuti Muzolowere
Mukasamukira Mumpingo Wina?
KODI munayamba mwasamukirapo kodi iye anatani kuti ‘Yehova amutsogolere panjira
mumpingo wina? Ngati ndi choncho yake’? Iye anati: “Mobwerezabwereza ndinkamufo-
tokozera Yehova za mantha amene ndinali nawo,
mukhoza kuvomereza zimene nkhawa zanga komanso kuti ndinkadziona kuti ndili
Jean-Charles ananena. Iye anati: ndekhandekha. Nthawi iliyonse ndikachita zimenezi,
“Zimakhala zovuta kuzolowera mpingo iye ankandipatsa mphamvu zimene ndinkafunikira.”
watsopano, pa nthawi yomweyo Kodi mungatani kuti muzidalira kwambiri Yehova?
Mofanana ndi mbewu imene imafunika madzi ndi
n’kumaonetsetsa kuti aliyense m’banja
zakudya zina za munthaka kuti ikule, chikhulupiriro
lanu akupitiriza kuchita zinthu zomwe chathu chimafunikanso zinthu zina kuti chikule. Ni-
zingalimbitse ubwenzi wake ndi Yehova.” colas yemwe tamutchula kale uja anapeza kuti ku-
Kuwonjezera pa kupeza ntchito, malo ganizira kwambiri za anthu monga Abulahamu, Yesu
okhala, mwinanso sukulu zatsopano, ndi Paulo, omwe analolera kusiya zinthu zambiri kuti
atumikire Mulungu, kunamuthandiza kuti azikhulu-
anthu omwe asamuka amafunika
kuzolowera nyengo yatsopano,
chikhalidwe china komanso gawo
latsopano lolalikira.
´
Nicolas ndi Celine anakumana ndi vuto la mtundu
wina. Iwo anavomera ofesi ya nthambi ya ku France
itawapempha kuti asamukire mumpingo wina. Iwo
anati: “Poyamba tinasangalala kwambiri koma ke-
nako tinayamba kuwasowa anzathu. Tinali tisanaya-
mbe kuzolowerana kwambiri ndi abale amumpingo
watsopanowu.” Ngakhale kuti pamakhala mavuto
ngati amenewa, kodi n’chiyani chingatithandize kuti
tizisangalalabe tikasamukira mumpingo watsopa-
no? Kodi ena angathandize bwanji? Nanga munga-
tani kuti muzilimbikitsidwa komanso kulimbikitsa
ena mumpingo watsopanowu?
MFUNDO 4 ZOMWE ZINGAKUTHANDIZENI
1. Muzidalira Yehova. (Sal. 37:5) Mlongo Kazumi
wa ku Japan, anasamuka mumpingo umene ana-
khalamo kwa zaka 20 pamene mwamuna wake ana-
sinthidwa kuti azikagwira ntchito kudera lina. Ndiye

 Mungapeze malangizo othandiza munkhani yakuti “Kulimba-


na ndi Malingaliro a Kulakalaka Kumudzi Kwanu mu Utumiki wa Muzidalira Yehova
Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1994.

26 NSANJA YA OLONDA
pirira kwambiri kuti Yehova amuthandiza. Kuphunzi-
ra Baibulo nthawi zonse kungakuthandizeni kuti
muzolowere zinthu zimene zasintha komanso kuti
mupeze zinthu zimene mungalimbikitse nazo ena
mumpingo wanu watsopano.
2. Muzipewa kuyerekezera. (Mlal. 7:10) Jules
atasamuka kuchoka ku Benin kupita ku United
States ankafunika kusintha kuti azolowere chikhali-
dwe china. Iye anati: “Ndinkafunika kufotokozera
munthu aliyense yemwe ndakumana naye koyamba
chilichonse chokhudza ineyo.” Popeza chikhalidwe-
chi chinali chosiyana ndi zimene anazolowera, ana-
yamba kupewa abale ndi alongo. Koma atawadziwa
bwino anasintha mmene ankawaonera. Iye anati:
“Tsopano ndikudziwa kuti kulikonse padzikoli anthu
ndi ofanana. Iwo amangolankhula kapena kuchita
zinthu mosiyana. Kuchita zinthu ndi anthu mogwiri-
zana ndi zimene anazolowera n’kofunika kwambiri.”
Choncho muzipewa kuyerekezera mpingo wanu wa-
kale ndi watsopano. Mpainiya wina dzina lake,
Anne-Lise, ananena kuti: “Sindinasamuke kuti ndi-
kapeze zofanana ndi zimene ndinasiya, koma kuti
ndikaphunzire zatsopano.”
Akulu ayeneranso kusamala kuti asamayerekeze-
re mpingo wawo wakale ndi watsopano. Ngati abale
akuchita zinthu m’njira yosiyana mumpingo watso- Muzipewa kuyerekezera
panowo si nthawi zonse pamene zimakhala kuti
akulakwitsa. Ndi nzeru kudziwa bwino mmene zi-
nthu zilili mumpingo watsopanowo musanapereke
maganizo anu. (Mlal. 3:1, 7b) Chitsanzo chanu cha- tsa ntchito nyumba yathu pochitiramo misonkhano
bwino chingathandize abale mumpingomo mmalo yokonzekera utumiki.”
mowakakamiza kuti azingotsatira maganizo anu. Kuyesetsa kuchita zinthu zokhudza kulambira
—2 Akor. 1:24. “mogwirizana” ndi abale ndi alongo mumpingo
3. Muzichita nawo zambiri. (Afil. 1:27) Kusamu- wanu watsopano, kudzakuthandizani kuti mupitiri-
ka ndi kotopetsa ndipo kumafuna nthawi yambiri. ze “kukhulupirira uthenga wabwino.” Anne-Lise,
Koma ngati n’kotheka, kuyambira pamene mwango- amene tamutchula kale uja analimbikitsidwa ndi
fika, muzisonkhana nawo pamasom’pamaso. Ndi- akulu kuti aziyesetsa kulalikira ndi aliyense mu-
po ngati abale ndi alongo mumpingo watsopanowo mpingo. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye ana-
samakuonani kapena amangokuonani mwa apo ndi ti: “Ndinazindikira kuti zimenezi zinandithandiza
apo, kodi angakuthandizeni bwanji? Lucinda, ndi kuti ndizolowere mofulumira.” Komanso kudzipe-
ana ake aakazi awiri, omwe anasamukira mumzinda reka pogwira nawo ntchito yokonza pa Nyumba ya
waukulu ku South Africa, anati: “Anzanga anandi- Ufumu kungasonyeze kuti tsopano mwayamba ku-
langiza kuti ndiyenera kumacheza kwambiri ndi ona kuti umenewu ndi mpingo wanu. Mukamachita
abale ndi alongo mumpingo watsopanowu, kumalo- nawo kwambiri zinthu limodzi abale ndi alongowo
wa nawo mu utumiki, komanso kumayankha pami- adzayamba kumasuka nanu ndipo mudzayamba
sonkhano. Tinauzanso abale kuti akhoza kumagwiri- kuwaona kuti ndi anthu a m’banja lanu lauzimu.

JULY 2024 27
Ndiye kodi mungatani kuti muthandize anthu
amene angosamukira kumene mumpingo wanu?
Mtumwi Paulo ananena kuti: “Muzilandirana. Ngati
mmene Khristu anatilandirira.” (Aroma 15:7) Potsa-
nzira Khristu, akulu angathandize anthu amene
angosamukira kumene mumpingo wawo kuti azidzi-
mva kuti alandiridwa. (Onani bokosi lakuti “Kodi
Mungatani Kuti Kusamuka Kusakhale Kovuta?”) Ko-
mabe, onse mumpingo, kuphatikizapo ana, anga-
thandize anthu amene abwera mumpingo kupeza
anzawo atsopano.
Kulandira ena kukuphatikizapo kuwaitana
kunyumba kwathu, komanso kuwathandiza pa
zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mlongo wina
anapeza nthawi yolowa m’tauni ndi mlongo amene
anali atangosamukira kumene mumpingo wawo kuti
akamuonetse malo ndiponso kokwerera mabasi.
Zimene anachitazo zinamuthandiza mnzakeyo kuti
azolowere mwamsanga.

ZIMATIPATSA MWAYI WOKULA MWAUZIMU


Chiwala chikamakula, chimafundula maulendo
Muzichita nawo zambiri angapo kuti mapiko amasuke n’kuyamba kuuluka.
Mofanana ndi zimenezi, inunso mukasamukira mu-

4. Muzipeza anzanu atsopano. (2 Akor. 6:11-


13) Kuchita chidwi ndi ena kungakuthandizeni
kuti mupeze anzanu atsopano. Choncho muzipeza
nthawi misonkhano isanayambe kapena itatha yoti
muzicheza ndi ena n’cholinga choti muwadziwe bwi-
no. Muziyesetsa kudziwa mayina awo. Kukumbukira
mayina a anthu komanso kukhala ochezeka, kunga-
thandize kuti ena azifuna kucheza nanu ndipo izi zi-
ngathandize kuti mupeze anzanu ambiri abwino.
M’malo modera nkhawa ndi kuchita zinthu
zinazake zapadera n’cholinga choti anthu akuko-
ndeni, muzilola kuti abale ndi alongo akudziweni
mmene mulili. Muzichita zimene Lucinda ananena.
Iye anati: “Panopa tili ndi anzathu abwino ambiri
chifukwa chakuti tinayamba ndife kuwaitanira ku-
nyumba kwathu.”
“MUZILANDIRANA”
Ena amachita mantha akalowa m’Nyumba ya Muzipeza anzanu atsopano
Ufumu yodzaza ndi anthu amene sakuwadziwa.

28 NSANJA YA OLONDA
mpingo watsopano, muyenera kukhala ngati mwa- kugwirizana ndi anzanu akale. Mungamathandize-
fundula popewa zilizonse zimene zingakulephere- nso amene abwera kumene kapena osowa powapa-
tseni kutumikira Yehova momasuka. Nicolas ndi tsa zimene akufunikira. Popeza chikondi ndi khali-
´ dwe lomwe limadziwikitsa Akhristu oona, kuchita
Celine ananena kuti: “Kusamuka kumatiphunzitsa
zinthu zambiri. Timafunika makhalidwe atsopano zimenezi kungakuthandizeni kuti mulimbitse ubwe-
kuti tizolowerane ndi anthu komanso malo atsopa- nzi wanu ndi Yehova. (Yoh. 13:35) Mungakhale otsi-
no.” Jean-Charles, amene tamutchula kumayambiri- mikiza kuti ‘Mulungu amasangalala ndi nsembe
ro uja anafotokoza mmene kusamuka kwathandizira zoterozo.’—Heb. 13:16.
banja lake. Iye anati: “Kusamuka kwathandiza kuti Ngakhale kuti pamakhala zovuta zina, Akhristu
ana athu azichita bwino mumpingo. Patangotha mi- ambiri zinthu zimawayendera bwino akasamukira
yezi yochepa, mwana wathu wamkazi anayamba ku- mumpingo wina, ndipo inunso zingakuyendereni
kamba nkhani pamisonkhano ya mkati mwa mlungu bwino. Anne-Lise ananena kuti: “Kusamukira mu-
ndipo mwana wathu wamwamuna anakhala wofali- mpingo wina kunandithandiza kuti ndidziwane ndi
tsa wosabatizidwa.” anthu ambiri.” Kazumi ananena motsimikiza kuti
Bwanji ngati simungathe kusamukira kwina, mo- “ukasamukira mumpingo wina umaona Yehova aku-
nga kukatumikira kumene kukufunika olalikira ambi- kuthandiza m’njira imene sunaiganizirepo.” Jules
ri? Mungachite bwino kutsatira malangizo omwe ananena kuti: “Anzanga amene ndapeza amandi-
takambirana munkhaniyi muli mumpingo wanu wo- thandiza kuti ndisamachitenso chilendo. Panopa
mwewo. Muzidalira Yehova ndipo muzichita zambiri ndimaona kuti ndine wamumpingomu, ndipo zidza-
mumpingo pokonza zoti muzilalikira ndi anthu ena, ndivuta kuti ndisamukemo.”
kupanga mabwenzi atsopano komanso kupitiriza

Kodi Mungatani Kuti Kusamuka


Kusakhale Kovuta?
Zimene muyenera kuchita: Muzilankhula ndi aku- Zimene akulu ayenera kuchita: Mlembi wa
lu a mipingo yonse iwiri nthawi idakalipo, n’kuwa- mpingo wanu wakale, ayenera kutumiza mwamsa-
fotokozera madeti omwe mudzasamuke, ndiponso nga kalata komanso Khadi Lolembapo Ntchito za
kuwapatsa adiresi yanu yatsopano ndi nambala Wofalitsa kumpingo watsopano. Komiti ya Utumi-
yanu ya foni. Muzifufuzanso kuti mudziwe pamene ki ya Mpingo watsopano iyenera kuika mwamsa-
pali Nyumba ya Ufumu komanso nthawi za miso- nga munthu amene wabwera kumene m’kagulu
nkhano. Mukafika pamisonkhano kwa nthawi yo- ka utumiki. Zingakhalenso bwino ngati woyang’a-
yamba muzidzidziwikitsa kwa akulu komanso nira kaguluko atakayendera komanso kulimbikitsa
abale ndi alongo. amene wabwera kumeneyo.

JULY 2024 29
MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA

Kodi “mkazi” wotchulidwa pa Yesaya 60:1 ndi ndani, nanga ‘anaimirira’


bwanji komanso anaonetsa bwanji “kuwala”?

ˇ Lemba la Yesaya 60:1, limati: “Imirira mkazi Koma maulosi a Yesaya onena za kubwezeretsa
iwe! Onetsa kuwala kwako, chifukwa kuwala anangokwaniritsidwa pang’ono pa nthawiyo. Aisi-
kwako kwafika. Ulemerero wa Yehova wakuuniki- raeli ambiri sanapitirize kumvera Mulungu. (Neh.
ra.” Nkhani yonse ikusonyeza kuti “mkaziyu” ana- 13:27; Mal. 1:6-8; 2:13, 14; Mat. 15:7-9) Pambu-
li Ziyoni kapena Yerusalemu, yemwe anali likulu la yo pake, anafika pokana Yesu Khristu, yemwe ndi
Yuda pa nthawiyo. (Yes. 60:14; 62:1, 2) Mzinda- Mesiya. (Mat. 27:1, 2) Mu 70 C.E., Yerusalemu ndi
wu umaimira mtundu wonse wa Isiraeli. Mawu kachisi wake anawonongedwa kachiwiri.
amene Yesaya ananenawa, akubweretsa mafunso Yehova anali ataneneratu kuti zimenezi zi-
awiri: Loyamba, ndi liti pamene Yerusalemu ‘anai- dzachitika. (Dan. 9:24-27) Choncho, sichinali
mirira’ ndiponso kuonetsa kuwala, nanga anachi- cholinga chake kuti Yerusalemu wa padziko lapa-
ta bwanji zimenezi? Lachiwiri, kodi mawu a nsi akwaniritse mbali iliyonse ya ulosi wa pa Yesa-
Yesayawa akukwaniritsidwanso kwambiri mu ya chaputala 60, wonena za kubwezeretsa.
nthawi yathu? Kodi mawu a Yesaya akukwaniritsidwanso
Ndi liti pamene Yerusalemu ‘anaimirira’ ndi- kwambiri mu nthawi yathu? Inde, koma akukwa-
ponso kuonetsa kuwala, nanga anachita bwanji niritsidwa pa mkazi wophiphiritsa, yemwe ndi
zimenezi? Pa nthawi imene Ayuda anali ku uka- “Yerusalemu wam’mwamba.” Ponena za mkazi-
polo ku Babulo kwazaka 70, Yerusalemu ndi ka- yu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndi mayi
chisi wake anali bwinja. Koma Ababulo atago- athu.” (Agal. 4:26) Yerusalemu wam’mwamba ndi
njetsedwa ndi Amedi ndi Aperisiya, Aisiraeli mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu, yomwe
omwe ankakhala m’madera onse olamuliridwa ndi angelo okhulupirika. “Ana” ake ndi Yesu ndi
ndi Ababulo anamasulidwa kuti abwerere kwawo Akhristu odzozedwa okwana 144,000, omwe mo-
fanana ndi Paulo, ali ndi chiyembekezo cha ku-
ndi kukabwezeretsa kulambira koona. (Ezara 1:
mwamba. Akhristu odzozedwawa amapanga
1-4) Kuyambira mu 537 B.C.E., anthu okhulupiri-
“mtundu woyera,” womwe ndi “Isiraeli wa Mulu-
ka amene anatsala m’mafuko onse 12, anabwe-
ngu.”—1 Pet. 2:9; Agal. 6:16.
rera. (Yes. 60:4) Iwo anayamba kupereka nsembe
Kodi Yerusalemu wam’mwamba ‘anaimirira’
kwa Yehova, kupanga zikondwerero ndiponso ku-
bwanji nanga anaonetsa bwanji “kuwala”? Iye
manganso kachisi. (Ezara 3:1-4, 7-11; 6:16-22)
anachita zimenezi kudzera mwa ana ake odzoze-
Apa ulemerero wa Yehova unayambiranso kuuni-
dwa a padziko lapansi. Tiyeni tione kufanana kwa
kira Yerusalemu, kutanthauza anthu a Mulungu
zimene zinawachitikira ndi zomwe zinaloseredwa
omwe anabwerera kwawo. Kenako nawonso ana-
pa Yesaya chaputala 60.
yamba kuwala pakati pa anthu amitundu ina
Akhristu odzozedwa anafunika ‘kuimirira’ chi-
amene sankadziwa Yehova.
fukwa anali mum’dima wophiphiritsa pa nthawi
 Pa Yesaya 60:1, Baibulo la Dziko Latsopano limagwiritsa imene mpatuko unafalikira atumwi onse atamwa-
ntchito mawu akuti “mkazi” osati “Ziyoni” kapena “Yerusale- lira. (Mat. 13:37-43) Choncho, iwo anali mu uka-
mu,” chifukwa mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti polo wa Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembe-
“imirira” komanso “onetsa kuwala,” amasonyeza kuti amene
akuuzidwayo ndi wamkazi, ngatinso mmene zilili ndi mawu aku- dzo zonse zabodza. Odzozedwa anakhala ali mu
ti “iwe.” ukapolowu mpaka “mapeto a nthawi ino,” omwe

30 NSANJA YA OLONDA
anayamba mu 1914. (Mat. 13:39, 40) Pasanapite Yerusalemu Watsopano adzachita zambiri po-
nthawi, mu 1919, iwo anamasulidwa ndipo ntha- kwaniritsa ulosi wa pa Yesaya 60:1. (Yerekezerani
wi yomweyo anayamba kuonetsa kuwala pogwira Yesaya 60:1, 3, 5, 11, 19, 20 ndi Chivumbulutso
ntchito yolalikira mwakhama. Kwazaka zonsezi, 21:2, 9-11, 22-26.) Yerusalemu wapadziko lapa-
anthu ochokera m’mitundu yonse akhala akutsa- nsi anali likulu la boma la Isiraeli wakale, cho-
tira kuwalaku kuphatikizapo anthu a Isiraeli wa ncho nayenso Yerusalemu Watsopano limodzi ndi
Mulungu amene anatsala, omwe ndi “mafumu” Khristu, adzakhala boma la ulamuliro watsopano.
otchulidwa pa Yesaya 60:3.—Chiv. 5:9, 10. Kodi Yerusalemu Watsopano akutsika bwanji “ku-
chokera kumwamba kwa Mulungu”? Akuchita zi-
M’tsogolomu, Akhristu odzozedwa adzaonetsa
menezi pochita zinthu zimene zikukhudza dziko
kwambiri kuwala kwa Mulungu. Kodi adzachita
lapansi. Anthu oopa Mulungu ochokera m’mitu-
bwanji zimenezi? Akadzamaliza utumiki wawo wa
ndu yonse ‘adzaunikiridwa ndi kuwala kwake.’ Iwo
padziko lapansi, iwo adzakhala mbali ya “Yeru-
adzamasulidwanso ku uchimo ndi imfa. (Chiv. 21:
salemu Watsopano” kapena mkwatibwi wa Khri-
3, 4, 24) Zotsatira zake n’zakuti ‘zinthu zonse zi-
stu, yemwe ndi mafumu ndi ansembe 144,000. dzabwezeretsedwa’ ngati mmene Yesaya ndi ane-
—Chiv. 14:1; 21:1, 2, 24; 22:3-5. neri ena ananenera. (Mac. 3:21) Kubwezeretsa
 Kubwezeretsedwa kwa kulambira koona komwe kunachitika kwakukulu kunayamba pamene Khristu anakhala
mu 1919 ndi kumene kwafotokozedwanso pa Ezekieli 37:1-14 ndi Mfumu ndipo kudzatha pamapeto pa Ulamuliro
Chivumbulutso 11:7-12. Ezekieli ananeneratu kuti Akhristu onse wa Zaka 1,000.
odzozedwa, adzamasulidwa mu ukapolo pambuyo pa nthawi
yaitali. Ulosi wa pa Chivumbulutso umanena za kubadwanso
kophiphiritsa kwa kagulu ka abale odzozedwa omwe anaya-
mbiranso kutsogolera pambuyo pokhala kwakanthawi asaku-
tha kutumikira Yehova bwinobwino chifukwa anamangidwa
mopanda chilungamo. Mu 1919,” iwo anaikidwa kukhala “kapo-
lo wokhulupirika komanso wanzeru.”—Mat. 24:45.

JULY 2024 31
34567 July 2024  Vol. 145, Na. 8 CHICHEWA ZOTI NDIPHUNZIRE
Muziphunzira Mwakhama
Kuti Mukhale Maso
M’MAGAZINIYI MULI
 Werengani Danieli 9:1-19 kuti muone
Nkhani Yophunzira 27: September 9-15 2 kufunika kophunzira mwakhama.

Muzikhala Olimba Mtima Ngati Zadoki Muziona nkhani yonse. Kodi ndi zinthu
ziti zomwe zinali zitangochitika kumene,

nanga zinamukhudza bwanji Danieli? (Dan.
Nkhani Yophunzira 28: September 16-22 8 5:29–6:5) Kodi mukanakhala Danieli muka-
namva bwanji?
Kodi Mumatha Kuzindikira Choonadi?
Muzifufuza mozama. Kodi ndi “mabuku opa-

tulika” ati omwe Danieli ankawerenga? (Dan.
Nkhani Yophunzira 29: September 23-29 14 9:2, mawu a m’munsi; w11 1/1 22 ˚2) N’chifu-
Tiyenera Kukhala Maso Kuti Tizipewa kwa chiyani iye analapa machimo ake koma-
nso a Aisiraeli onse? (Lev. 26:39-42; 1 Maf. 8:
Mayesero
46-50; dp 182-184) Kodi pemphero la Danieli
 likusonyeza bwanji kuti ankaphunzira Mawu a
Nkhani Yophunzira 30: September 30–October 6 20 Mulungu mwakhama?—Dan. 9:11-13.

Zimene Tikuphunzira kwa Mafumu a Chiisiraeli Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni


kuti:


Kodi Mungatani Kuti Muzolowere ˙ ‘Kodi ndingatani kuti ndisasokonezedwe


Mukasamukira Mumpingo Wina? 26 ndi zochitika za m’dzikoli?’ (Mika 7:7)


˙ ‘Kodi kuphunzira Baibulo mwakhama ngati
mmene Danieli ankachitira kunganditha-
MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA 30 ndize bwanji?’ (w04 8/1 12 ˚17)
˙ ‘Kodi ndi nkhani ziti zomwe ndingaphunzire
zimene zingandithandize “kukhalabe
maso”?’ (Mat. 24:42, 44; w12 8/15 5 ˚7-8)

Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu


Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene
anthu amapereka mwakufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka pitani pa
donate.jw.org.
Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la
Malemba Opatulika lolembedwa m’Chichewa chamakono, kupatulapo ngati Pitani pawebusaiti ya jw.org, kapena pangani
tasonyeza Baibulo lina. sikani kachidindo aka

s
The Watchtower (ISSN 0043-1087) July 2024 is published by Watchtower
Bible and Tract Society of New York, Inc.; Harold L. Corkern, President; Mark
L. Questell, Secretary-Treasurer; 1000 Red Mills Road, Wallkill, NY 12589-
w24.07-CN

3299, and by Watch Tower Bible and Tract Society of South Africa NPC, 1 Ro-
240227

bert Broom Drive East, Rangeview, Krugersdorp, 1739. ˘ 2023 Watch Tower
Bible and Tract Society of Pennsylvania. Printed in South Africa.

You might also like