Jump to content

Akafula

From Wikipedia
Akafula akuvina gule wa Baka kummawa kwa dziko la Cameroon
A Batwa akuvina ku Uganda

Akafula kapena a batwa omwe pa chizungu amati ma pygmy ndi anthu osiyanasiyana a pakati pa dera la Africa amene kutalika kwawo sikuposa 150cm (4 ft 11 in). Anthu a chi Negrito a ku Asiandi ena aliwonse aafupi amatchedwanso kuti akafula. Eni akewo sasangalala kutchudwa pa dzina limeneli koma dzina lawo lina lomwe lili lonyoza kwambiri ndi amwandiwonerapati.

Akafula amatchedwa ndi dzina loti a Bayaka ku Central African Republic, kapena a Bambenga ku Congo.

Komwe Kunachokela Akafula

[Sinthani | sintha gwero]

Anthu ambiri amakhulupilira kuti Akafuna ndi zidzukulu za anthu amaene ankakhala ku nkhalango za pakati pa Africa amene anasamutsidwa ndi kulowelerana ndi kusamuka kwa anthu okonda kulima a ku Sudan ndi a chi Bantu. Maganizo amenewa alib eumboni weniweni wa anthu ofufuza za mbiri ya kale, ndipo ofufuza za chilankhulo ndi kumene kunachokera anthu amakayikira zimenezi. [1][2][3]

Pali malo okhudza za mitengo komanso zoyenga uchi pakati pa akafula a ku Cameroon ndi ku Gabon ngakhale zilankhulo zawo zili zosiyana. Izi zimasonyeza kuti anthuwa anachokera kumodzi.

Matupi ndi chilengedwe cha Akafula a kummawa kumasiyana ndi anthu a mayiko ena. Iwowa ndi aafupi kuposa Akafula ena, kusonyeza kuti ndi akale kwambiri kuponsa Akafula onse. Iwowa chiyambi chawo chimafanana ndi a Hadzabel, amene amakhala kummawa kwa nkhalango ya pakati pa Africa amene anali aafupi kwambiri koma chifukwa choyandikana ndi kukwatirana ndi anthu aatali amene anayandikana nawo, anasintha kutalika kwawo. Akafula ena amene chilengedwe chawo chinayesedwa samasiyana ndi anthu oyandikana nawo amene si Akafula, kutanthauza kuti chilengedwe chawo chinasinthika pobelekerana ana ndi anthu amene sali akafula, kapenaso kuti ndo wosiyana ndi a Mbuti. Anthu ena a sayansi amakhulupilira kuti akafula enawa ndi amodzi ndi anthu a chi Bantu amene anayamba kupita ku nkhalango ya pakati pa Africa.

Anthu ofufuza za chilengedwe cha anthu amaganiza kuti Akafula amakhala aafupi chifukwa chosowa chakudya mu nkhalango, kusowa zofunikira zina ngati calcium mu nthaka, komanso kuti matupi awo amasintha mainga ndi malo amene amakhalawo ndi kubereka nsanga chifukwa chakuti amamwaliranso msanga.[4]

Akafula amakhalanso mu nkhalango mmene dzuwa silimalowa bwino bwino, zomwe zimapangitsa kuti akhale a mafupa ang'ono ang'ono. [5] [6]

Wanu Oscar

Kuphedwa kwa Akafula

[Sinthani | sintha gwero]

Pa nkhondo yachiwiri ya ku Congo, akafula ankasakidwa ngati zinyama ndipo ankadyedwa. Anthu amene ankachita nkhondoyi ankaawona ngati Akafulawo si anthu ndipo ena ankayesa kuti nyama ya akafula imapeleka mangolomera. Ogwira ntchito a ku United Nations amene amateteza ufulu wa anthu analengeza mu 2003 kuti anthu otsutsa boma anka

  1. R. Blench and M. Dendo. Genetics and linguistics in sub-Saharan Africa, Cambridge-Bergen, June 24, 2004.
  2. Klieman, Kairn A. The Pygmies Were Our Compass: Bantu and BaTwa in the History of West Central Africa, Early Times to c. 1900, Heinemann, 2003.
  3. Cavalli-Sforza, Luigi Luca, ed. African Pygmies. Orlando, Fla.: Academic Press, 1986
  4. [1]
  5. "Archive copy". Archived from the original on 2003-12-30. Retrieved 2008-02-15. Unknown parameter |dead-url= ignored (help)CS1 maint: archived copy as title (link)
  6. O'Dea, JD. Possible contribution of low ultraviolet light under the rainforest canopy to the small stature of Pygmies and Negritos. Homo: Journal of Comparative Human Biology, Vol. 44, No.3, pp. 284-7, 1994